settings icon
share icon
Funso

Kodi ziweto / nyama zimapita Kumwamba? Kodi ziweto / nyama zili ndi mizimu?

Yankho


Baibulo silipereka yankho mwatsatanetsatane pa nkhani iyi ya kuti nyama zosungidwa kapena nyama zili ndi “mzimu” kapenanso kuti zidzakhalako kumwamba. Koma titha kuwerenga bwino Mau a Mulungu ndi kudziwa zambiri pa nkhani iyi. Baibulo linena kuti anthu (Genesis 2:7) ndi nyama (Genesis 1:30; 6:17; 7:15, 22), zili ndi “umoyo wopuma”; kunena kuti anthu ndi nyama ndi zolengedwa za moyo. Kusiyana kwakukuru kumene kulipo pakati pa anthu ndi nyama ndi kwakuti anthu anapangidwa mcifaniziro ca Mulungu (Genesis 1:26-27), pamene nyama sizinapangidwe tero. Kupangidwa mcifaniziro ca Mulungu kutsimikiza kuti anthu ali monga Mulungu, okhala ndi mzimu, wopembeza, acifuno, ndipo ali ndi mbali ya umoyo wao imene ipitiliza akafa. Ngati nyama ziri ndi “mzimu” wopanda maonekedwe, pamenepa ndiko kuti izo sizili pa myeso wa munthu ai, muyeso wake ndiwocepekera. Kusiyana kumeneku mwina kutanthauza kuti ngkhale kuti ziri ndi “mzimu” koma supitilira zikafa.

Cina coganizirapo ndi cakuti nyama nazonso zinalengedwa ndi Mulungu ndipo zili gawo la cilengedwe cake. Mulungu analenga nyama ndipo anati zinali zabwino (Genesis 1:25). Motero palibe cifukwa cakuti pa dziko latsopano sipadzakhala nyama (Chibvumbulutso 21:1). Cioneka bwino kuti pa nthawi yomweyo ya zaka cikwi cimodzi (1000), nthawi ya mtsogolo yomwe aliyense adzakondwera nayo, nyama nazonso zidzakhalako pa nthawiyi (Yesaya 11:6; 65:25). Koma ndicovuta kunena motsimikiza kuti zina mwa nyama izi zidzakhala zosungidwa m’manja ya anthu pa nthawi imeneyo yakukhala padziko. Tidziwa kuti Mulungu ndi wacilungamo ndiponso kuti tikakafika kumwamba, tidzazipeza tili mcipangano ca Mau ake titabvomereza monga ananenera kale pa nkhani iyi.

EnglishBwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi ziweto / nyama zimapita Kumwamba? Kodi ziweto / nyama zili ndi mizimu?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries