settings icon
share icon
Funso

Mwakhululukidwa? Ndingakhululukidwe bwanji ndi Mulungu?

Yankho


Funso: Mwakhululukidwa? Ndingakhululukidwe bwanji ndi Mulungu?

Yankho: Machitidwe a Atumwi 13:38 akuti, “Kotero, abale anga, ndikufuna inu mudziwe kuti kudzera mwa Yesu kukhulukidwa kwa machimo kudzadza kwa inu.”

Kodi chikhululuko ndi chani ndinso ndi chifukwa ninji ndikuchifuna?

Mau akuti “khululuka” akutanthauza kufufuta, kuchotsa mangawa, kufufuta ngongole. Tikawalakwira wena, timafuna chikhululuko chawo ndi cholinga chakuti ubale wathu ubwelere. Chikhululuko chimaperekedwa osati chifukwa chakuti munthu ayenera kukhululukidwa chabe. Palibe amene ayenera kukhululukidwa. Kukhululuka ndi chikondi chabe, chifundo, ndi chisomo. Kukhululuka ndi ganizo losafuna kusunga mangawa ndi munthu, posaganizira chomwe wakulakwira.

Baibulo limatiuza kuti tonse tikufuna Mulungu atikhululukire. Tonse tinalakwapo. Mlaliki 7:20 akunena, “Pakuti palibe wolungama pansi pano amene achita zabwino osachimwa.” Machimo onse ndi mchitidwe otsutsanandi Mulungu (Masalimo 51:4). Zotsatira zake, timafunafuna kukhululukidwa ndi Mulungu mothodwa. Ngati machimo athu sanakhululukidwe, tidzakhala tikumva zowawa chifukwa cha machimo athu (Mateyu 25:46 ; Yohane 3:36).

Kukhululuka – Tingakupeze bwanji?

Mothokoza, Mulungu ndi wachikondi ndi wachifundo – okonzeka kutikhululukira ife machimo athu! 2 Petro 3:9 akutiuza kuti, “… ali wodekha ndi inu, kotero anadzipereka chifukwa cha machimo athu.

Mphotho yokhayo ya tchimo ndi imfa. Theka loyamba la Aroma 6:23 likuti, “Mphotho ya tchimo ndi imfa …” Imfa yamuyaya ndiyomwe tapindula mumachimo athu. Mulungu, mudongosolo lake langwiro, anakhala munthu – Yesu Khristu (Yohane 1:1,4). Yesu anafa pamtanda, kutenga chilango chimene chinali chathu – imfa. 2 Akorinto 5:21 imatiphunzitsa kuti, “Mulungu anapanga Iye amene sanadziwe uchimo anamuyesera uchimo m’malo mwathu, ndi cholinga chakuti mwa Iye tikhale m’choonadi cha Mulungu.” Yesu anafa pamtanda, chifukwa cha machimo athu! Monga Mulungu, imfa ya Yesu inakhululukitsa machimo a dziko lonse lapansi. 1 Yohane 2:2 akunena kuti, “Iye ndiye chiwombolo cha machimo athu, koma osati athu okha komanso a dziko lonse lapansi.” Yesu anauka kwa akufa, kugonjetsa tchimo ndi imfa (1 Akolose 15:1-28). Tamandani Mulungu, kudzera mu imfa ndi kuuka kwa Yesu Khristu, theka lachiwiri la Aroma 6:23 ndiloona, “… koma mphatso ya Mulungu ndi moyo wosatha kudzera mwa Yesu Khristu Mulungu wathu.”

Kodi mukufuna machimo anu atakhululukidwa? Kodi muli ndi nkhawa mwakuti mukusowa mtendere? Kukhululukidwa kwa machimo anu kulipo ngati mwayika chikhulupiliro chanu mwa Yesu Khristu ngati Mpulumutsi wanu. Aefeso 1:7 akuti, “Mwa Iye tawomboledwa mu mwazi wake, kukhululukidwa kwa machimo, mongamwa kulemera kwa chisomo chake.” Yesu anapereka ngongole yathu, ndi cholinga chakuti tikhululukidwe. Chongoyenera kuchita ndikupempha Mulungu kuti akukhululukireni kudzera mwa Yesu, kukhulupilira kuti Yesu anafa kuti inu mukhululukidwe – ndipo Iye adzakukhululukirani! Yohane 3:16-17 ali ndi uthenga wabwinowu, “Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero kuti anatumiza mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wokhulupilira iye asatayike koma akhale nawo moyo wosatha. Pakuti Mulungu sanatumize mwana wake pa dziko lapansi kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi likapulumutsidwe ndi Iye.

Kukhululuka – ndikosavutadi?

Inde, ndikosavuta! Simungalandire chikhululuko kuchokera kwa Mulungu. Simungalipire chifukwa cha kukhululuka kwanu kuchokera kwa Mulungu. Mukhonza kungolandira, mwa chikhulupiliro, kudzera mwa chisomo ndi chifundo cha Mulungu. Ngati mukufuna kulandira Yesu Khristu kukhala Mpulumutsi wanu ndikulandila chikhululuko kuchokera kwa Mulungu, ili ndi pemphero limene mungapemphere. Kunena pemphero ili kapena pemphero liri lonse sikungakupulumutseni. Ndikukhulupilira mwa Yesu kokha kumene kungakupulumutseni ku machimo. Pemphero ili ndilongosonyeza kwa Mulungu chikhulupiliro chanu mwa Iye ndikumuthokoza pakukupatsani za chipulumutso chanu. “Mulungu, ndikuzindikira kuti ndakulakwirani ndipo ndili oyenera chilango. Koma Yesu Khristu anachitenga chilango chimene chinali choyenera ine kotero kuti mwa chikhulupiliro mwa Iye ndikhonza kukhululukiridwa. Ndikuyika chikhulupiliro changa mwa inu kuti ndikapulumuke. Zikomo chifukwa cha chisomo chanu chodabwitsa ndi kukhululuka kwanu! Amen!”

Kodi mwapanga ganizo la Khristu chifukwa cha zimene mwawerenga pano? Ngati ndi choncho, chonde sindikizani batani la “Ndavomera kulandira Khristu lero” pansipa.

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Mwakhululukidwa? Ndingakhululukidwe bwanji ndi Mulungu?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries