settings icon
share icon
Funso

Kodi Yesu ndi Mulungu? Kodi Yesu ananenapo kuti Iye ndi Mulungu?

Yankho


Yesu sanalembedwepo mu Baibulo kuti anenapo mawu akuti, “Ine ndine Mulungu.” Izi sizikutanthauza, komabe, kuti sanadzitchule kuti Iye ndi Mulungu. Mwachitsanzo mawu a Yesu mu Yohane 10:30, “Ine ndi Atate ndife amodzi.” Tikuyenera kungoona machitidwe a Ayuda pa mawu ake kuti tidziwe kuti amadzitchula Mulungu. Anafuna kumugenda miyala chifukwa cha chifukwa chomwechi. “… inu, muli munthu, mudziyesera nokha Mulungu” (Yohane 10:33). Ayuda anazindikira bwino lomwe zimene Yesu anali kunena – m’modzi mwa Milungu. Dziwani kuti Yesu samakana kuti amadzitchula Mulungu. Pamene Yesu ananena, “Ine ndi Atate ndife amodzi” (Yohane 10:30), amanena kuti Iye ndi Atate ndi achikhalidwe chimodzi. Yohane 8:58 ndi chitsanzo china. Yesu anati, “Indetu, indetu, ndinena kwa inu, asanayambe kukhala Abrahamu, ine ndilipo!” Kuyankha kwa Ayuda amene anamva mawu awa kunali kutenga miyala ndikumupha Iye chifukwa cha mwano, monga m’mene lamulo la Mose liwalamulira iwo kuchita (Levitiko 24:15).

Yohane anabwereza maganizo a Yesu a M’modzi mwa Milungu: “Mawu anali Mulungu” ndi “Mawu anasandulika thupi” (Yohane 1:1,14). Ndime zimenezi zikuonetseratu poyera kuti Yesu ndi Mulungu mu Thupi. Machitidwe a Atumwi 20:28 akutiuza kuti, “Khalani otsogolera Mpingo wa Mulungu, umene anagula ndi mwazi wake.” Ndi ndani amene anagula Mpingo – Mpingo wa Mulungu – ndi mwazi wake? Yesu Khristu. Machitidwe a Atumwi 20:28 akunena kuti Yesu anagula Mpingo wake ndi magazi ake. Kotero, Yesu ndi Mulungu!

Thomasi wophunzira wa Yesu ananena kwa Yesu nati, “Ambuye wanga ndi Mulungu wanga” (Yohane 20:28). Yesu sanamukonza iye. Tito 2:13 akutilimbikitsa kudikilira kubwera kwake kwa Mulungu ndi Mpulumutsi wathu, Yesu Khristu (onaninso 2 Petulo1:1). Pa Aheberi 1:8, Atate akunena za Yesu, “Koma ponena za Mwana anati, ‘Mpando wa chifumu wanu, Mulungu, ufikira nthawi za nthawi, ndipo oyera mtima adzakhala ndodo ya chifumu ya ufumu wanu.” Atate amafanizira kwa Yesu ngati “Mulungu” kuonetsa kuti Yesu ndiyedi Mulungu.

Ku Chivumbulutso, m’ngelo anauza Mtumwi Yohane kupembedza Mulungu yekha (Chivumbulutso 19:10). Nthawi zambiri mu Malembo Oyera Yesu amalandira matamando (Mateyu 2:11, 14:33, 28:9, 17; Luka 24:52; Yohane 9:38). Samadzudzula anthu chifukwa chakumupembedza Iye. Ngati Yesu sanali Mulungu, akatha kuwauza anthu kuti asamupembedze Iye, monga m’mene m’ngelo ku Chivumbulutso anachitira. Pali ndime zina za Malembo Oyera zambiri zimene zimanena za Yesu kukhala M’modzi mwa Milungu.

Chifukwa chofunikira kwambiri chakuti Yesu ayenera kukhala Mulungu ndi chakuti ngati sali Mulungu, imfa yake siikadakhala yokwanira kuwombolera machimo a dziko lapansi (1 Yohane 2:2). Munthu wolengedwa, amene Yesu adakakhala akanakhala kuti Iye si Mulungu, sakanalipira chilango cha muyaya choyenera tchimo limene walakwira Mulungu wamuyaya. Ndi Mulungu yekha angalipire chilango cha mtundu umenewu. Ndi Mulungu yekha amene angasenze machimo a dziko lapansi (2 Akolose 5:21), kufa, ndi kuuka, kugonjetsa tchimo ndi imfa.

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi Yesu ndi Mulungu? Kodi Yesu ananenapo kuti Iye ndi Mulungu?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries