settings icon
share icon
Funso

Kodi Mulungu alipo? Pali umboni kuti Mulungu alipo?

Yankho


Zikhonza kukhala ndi umboni kapena opanda umboni kuti Mulungu alipo. Baibulo likutiuza kuti tivomereze ndi chikhulupiliro kuti Mulungu alipo: “Ndipo opanda chikhulupiliro ndikosathekera kumukondweretsa Mulungu, chifukwa aliyense amene abwera kwa Iye ayenera kukhulupilira kuti Iye alipo ndikuti amapereka mphotho kwa iwo akumufunafuna Iye” (Aheberi 11:6). Ngati Mulungu afuna, akhonza kuonekera mosavuta ndikutsimikizira dziko lapansi kuti Iye alipo. Koma ngati achita chomwecho, sipadzakhala chifukwa chokhulupilira. “Ndipo Yesu ananena naye, ‘Chifukwa wandiona ine, wakhulupilira; odala iwo akhulupilira angakhale sanaone.

Zimenezi sizitanthauza, komabe, kuti palibe umboni kuti Mulungu alipo. Baibulo likuti, “Zakumwamba zimalalikira ulemelero wa Mulungu; Mitambo iwonetsa ntchito za manja ake. Usana ndi usana uchulukitsa mau; ndipo usiku ndi usiku uonetsa nzeru. Palibe chikhalidwe kapena mau pamene liu lawo silimveka. Muyeso wawo wapitilira pa dziko lonse lapansi, ndipo mau awo kumapeto kwa dziko” (Masalimo 19:1-4). Kuyang’ana nyenyezi, kudziwa kukula kwa mlengalenga, kuona zodabwitsa za chilengedwe, kuona kukongola kwa dzuwa – zinthu zonsezi zikuloza kwa Mulungu Mlengi. Ngati zimenezi zili zopelewera, palinso umboni wa Mulungu m’mitima mwathu. Mlaliki 3:11 akutiuza ife, “…Iye waikanso muyaya m’mitima mwawo.” Mkati mwa mitima yathu mukuzindikira kuti pali china chake patsidya pa moyo uno ndi wina wake patsidya pa dziko lino. Tikhonza kukana mwanzeru ngati sitikudziwa kanthu, koma kupezeka kwa Mulungu mwa ife ndi onse otizungulira ndizachidziwikire. Ngakhale zili chomwechi, Baibulo likutichenjeza kuti ena adzakanabe kuti Mulungu alipo: “Opusa amanena mumtima mwake kuti, ‘Kulibe Mulungu’ (Masalimo 14:1). Popeza anthu ambiri mumbiri yonse, mu zikhalidwe zonse, m’mitundu yonse, ndi m’maiko monse amakhulupilira mu milungu ina, pakuyenera kukhala china chake (kapena wina wake) oyambitsa chikhulupiliro chimenechi.

Kuphatikizapo pa mitsutso ya Baibulo ngati Mulingu alipo, pali mitsutso yoyenera kulingalira. Poyamba, pali mtsutso wokhudzana ndi kukhala kwa munthu ndi chinthu. Njira yotchuka kwambiri ya mtsutso wa kakhalidwe ka munthu ndi chinthu imagwiritsa ntchito ganizo la Mulungu potsimikiza kuti Mulungu alipo. Imayamba ndi kutanthauzira Mulungu ngati “wa moyo woposa chili chonse mungaganizire.” Kenaka pamakhala kutsutsana kuti Mulungu alipo kuposa kuti Mulungu kulibe, kotero kuti Munthu wamkulukulu akuyenera kuti alipo. Ngati Mulungu kulibe, ndiye kuti Mulungu sakadakhala Wamoyo ndi Wamkulukulu, ndikuti zikadasokoneza tanthauzo la Mulungu.

Mtsutso wachiwiri ndi mtsutso wophunzitsa kapena wokhulupilira kuti zochitika ndi chitukuko zimapangika malinga ndi cholinga ndi makonzedwe a anthu osati makina ayi. Mtsutso wophunzitsa kapena wokhulupilira kuti zochitika ndi chitukuko zimapangika malinga ndi cholinga ndi makonzedwe a anthu osati makina ayi umanena kuti popeze mlengalenga ndiokongola molapitsa, payeneka kukhala opanga wa umulungu. Mwachitsanzo, dziko lapansi likadakhala pafupi kapena kutali ndi dzuwa, silikadatha kuthandiza miyoyo yambiri yomwe panopa likuthandiza. Zofunikira mlengalenga mwathu zikadasiyana pang’ono, pafupifupi chamoyo chili chonse padziko lapansi chikhonza kufa. Zodabwitsa za kachakudya komanga thupi kochepa kwambiri komwe kangathe kugawa chinthu koma osasintha chilengedwe chake kopezeka mwamwayi ndi kamodzi mu 10243 (imene ili 10 motsogozana ndi ziro 243). Gawo limodzi laling’ono kwambiri la chinthu chamoyo lili ndi zofunikira zazing’ono zochuluka kwambiri zedi.

Mtsutso wachitatu woyenera kulingalira ngati Mulungu alipo umatchedwa mtsutso wa chiyambi cha dziko ndi chilengedwe chonse ndi kusintha kwake. Gwero lili lonse lili ndi chiyambi chake. Mlengalenga ndi zonse zili m’menemo ndi gwero. Payeneka kukhala china chake chiyambitsa chili chonse kuti chikhalepo. Potsilizira pake, payeneka kukhala china chake “chosayambitsa” ndicholinga choyambitsa zinthu zonse kukhalapo. Izo za “chosayambitsa” oyamba ndi Mulungu.

Mtsutso wachinayi umadziwika kuti mtsutso wa chikhalidwe. Mtundu uliwonse mu mbiri yake umakhala ndi malamulo ake. Aliyense amakhala ndi chikumbumtima. Kupha, kunama, kuba, ndi makhalidwe osayenera ndiosavomerezeka pafupifupi pena pali ponse. Kodi chikumbumtima chimenechi chinachokera kuti ngati kusali kwa Mulungu Oyera?

Ngakhale zinthu zili chomwechi, Baibulo limatiuza kuti anthu zachidziwikire za Mulungu m’malo mwale adzakhulupilira bodza. Aroma 1:25 akutiuza kuti, “iwo anasandutsa choonadi cha Mulungu kukhala chabodza, napembedza ndikutumikira zolengedwa ndikusinya Wolengayo – amene ali otamandika ku nthawi zosatha. Amen.”Ndiponso Baibulo limalalika kuti anthu alibe chowiringula posakhulupilira mwa Mulungu: “Pakuti chilengeleni dziko lapansi kusaoneka kwa Mulungu – mphamvu yake ndi umulungu wake – zakhala zikuonekera poyera, kumveka bwino kuchokera pazopangidwa, ndicholinga chakuti anthu asakhale ndipothawira” (Aroma 1:20).

Anthu amakana kuti Mulungu alipo chifukwa ndi “zosakhudzana ndi phunziro la sayansi” kapena “chifukwa palibe umboni.” Chifukwa choona ndichoti akangovomereza kuti Mulungu alipo, akuyeneranso kudziwa kuti ali ndi udindo kwa Mulungu ndikufuna kuti Mulungu awakhululukire machimo awo (Aroma 3:23, 6:23). Ngati Mulungu alipo, ndiye kuti Iye amalemba zochita zathu. Ngati Mulungu kulibe, ndiye tikhonza kuchita chili chonse chomwe tafuna popanda kudandaula kuti Mulungu adzatiweruza. Ndichifukwa chake ambiri mwa iwo amene amakana kuti Mulungu alipo amakakamira kwambiri pa ganizo la kusintha kwa chilengedwe – limawapatsa njira ina yokhulupilira mwa Mulungu Namalenga. Mulungu alipo ndipo mwachidziwikire aliyense amadziwa kuti Mulungu alipo. Pa chifukwa chakuti anthu ena amayesetsa kupanga makani ndi kupeza zifukwa zoonetsa kuti Mulungu kulibe ndikungosonyezeratu kuti ndi mkangano woonetsa kuti Mulungu alipo.

Timadziwa bwanji kuti Mulungu alipo? Monga a Khristu, timadziwa kuti Mulungu alipo chifukwa timalankhula naye tsiku liri lonse. Sitimamumva Iye akutilankhula ife, koma timadziwa kuti Mulungu wafika pakati pathu, timamva utsogoleri wake, timadziwa chikondi chake, timafuna chisomo chake. Zinthu zachitika m’miyoyo yathu zimene sitingazilongole koposa Mulungu. Mulungu watipulumutsa modabwitsa ndikusintha miyoyo yathu mwakuti sitingachitire mwina koma kuvomereza ndikumutamanda Iye. Palibe mwa mikangano imeneyi imene inganyengerere munthu amene akukana kuvomereza zinthu zimene zili zachidziwikire. Pamapeto pake, zakuti Mulungu alipo zivomerezedwa mwachikhulupiliro. (Aheberi 11:6). Chikhulupiliro mwa Mulungu tumphatumpha wosaona mumdima; ndi kwelero lotchinjirizidwa lolowera m’chipinda chowala bwino momwe anthu ambiri ayimilira kale.

EnglishBwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi Mulungu alipo? Pali umboni kuti Mulungu alipo?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries