settings icon
share icon
Funso

Kodi makhalidwe a Mulungu ndi otani? Kodi Mulungu ali bwanji?

Yankho


Nkhani yabwino ndiyakuti, pamene tiyesetsa kuyankha funso ili, tidziwe kuti pali zambiri zimene tingathe kupeza zonena kapena zokhuza Mulungu! Iwo amene afuna kumvetsa za ici, adzafuna kuti athandizike powerenga gawo lonse limeneli, ndi kulinganiza ndi Mau posanthula kuti amvetse bwino. Mau ochulidwa kapena kuti mabuku ochulidwa ndi wofunikira kwambiri pothandiza, pakuti popanda mphamvu ya Mau a Mulungu ndiko kuti zolembedwa izi zones zikhala cabe maganizo a munthu, cimene mwa ico ndicolakwika ndipo cosayenera ndiponso sitikhoza kumvetsa Mulungu (Yobu 42:7). Kunena kuti ndicofunikira kwa ife kumvetsa Mulungu ndi zosathekera popeza sitikhoza kum’mvetsa Iye ndi kunena zoona zenizeni ndicosatheka. Kulephera kutero kutha kutitaikitsa pamaso pace ndi kuyamba kupembedza milungu ina, cinthu cimene Iye Mulungu safuna (Eksodo 20:3-5).

Zokhazo zimene Mulungu wasankha kuti aziululire kwa anthu ndizo zidzadziwika. Cimodzi ca zikhalidwe za Mulungu ndi “kuwala,” kutanthauza kuti Iye amadziulula yekha (Yesaya 60:19; Yakobo1:17). Popeza Mulungu watiululira ife za Iye yekha tiyenera kuzisunga (Ahebri 4:1). Cilengedwe, Baibulo, ndi Mau a Mulungu osandulika thupi (Yesu Kristu) zidzatithandiza if kudziwa m’mene Mulungu ali.

Tiyeni tiyambe podziwa ndi kubvomereza kuti Mulungu ndiye anatilenga ndipo ife ndife gawo la cilengedwe cace (Genesis 1:1; Masalmo 24:1) ndipo tinapangidwa m’cifaniziro cace. Munthu asiyana ndi zina zonse zolengedwa popeza munthu anampatsa mphamvu ya kuyanganira pa zolengedwa zokhalira (Genesis 1:26-28). Cilengedwe cinaipitsidwa ndi ucimo pamene munthu anacimwa koma cionetsabe mbali ya nchito ya Mulungu (Genesis 3:17-18; Aroma 1:19-20). Poona pa kukula ndi kuchuluka kwa cilengedwe, koma kwace, ndi kusiyana kwace, m’menemo tionamo kukoma kwa Mulungu.

Zina zambiri za cikhalidwe ca Mulungu zidziwika mwa kuwerenga mau onena za maina ace a Mulungu. Ena mwa mauwo ndi awa:

Elohim – Wopambana, umulungu wace (Genesis 1:1)
Adonai – Ambuye, kuonetsa ubale umene umakhalapo pakati pa kapolo kapena wanchito ndi ambuyake (Eksodo 4:10, 13)
El Elyon - Mulungu Wamkurukuru, wopambana (Genesis 14:20)
El Roi - Wopambana Mulungu wakundiona ine (Genesis 16:13)
El Shaddai – Mulungu Wamphamvuyonse (Genesis 17:1)
El Olam – Mulungu wacikhalire (Yesaya 40:28)
Yahweh – AMBUYE, “INE NDINE,” kutanthauza wosatha ndi wokhalako yekha (Eksodo 3:13, 14).

Mulungu ndi wamuyaya, kutanthauza kuti alibe ciyambi ndipo alibe malekezero, ndiwokhalako ku nthawi zonse. Iye akhala muyaya ku nthawi zonse (Deuteronomo 33:27; Masalmo 90:2; 1 Timoteo 1:17). Mulungu sasinthika, kutanthauza kuti Iye akhalabe cimodzimodzi nthawi zonse motero Iye ndiodalirika pa zonse, titha kumukhulupirira Iye (Malaki 3:6; Numeri 23:19; Masalmo 102:26, 27). Mulungu sayelekezeka, kulibe wina wofanana ndi Iye pa zinchito zake kapena pa khalidwe lake. Iye sangalinganizidwe komanso ndi wambambande (2 Samueli 7:22; Masalmo 86:8; Yesaya 40:25; Mateyu 5:48). Mulungu ndi wosamvetsetseka,amene mwa nzeru za umunthu sikotheka kum’dziwa Iye mwakuya, amene sitingathe kukumba kapena kupeza kapena kulondola zake zonse (Yesaya 40:28; Masalmo 145:3; Aroma 11:33, 34).

Mulungu ndi wolungama; Iye sakondera munthu wina aliyense ai (Deuteronomo 32:4; Masalmo 18:30). Mulungu ndi Wamphamvuyonse; mwa mphamvu yace, iye akhoza kucita cina ciriconse comkomera; koma zocita zake sizizakangana ndi mkhalidwe wake ai (Chibvumbulutso 19:6; Yeremiya 32:17, 27). Mulungu ali pali ponse; Iye apezeka pa malo pena pali ponse koma kutero sikutanthauza kuti Mulungu ndi cina ciriconse (Masalmo 139:7-13; Yeremiya 23:23). Mulungu ndi Kadziwedziwe; Iye adziwa zonse, zakumbuyo, zatsopano ndi zam’tsogolo kuikapo ndi zonse zimene tingaganizire pa nthawi ina iriyonse. Pakuti Iye adziwa zonse, ciweruzo cace cidzacitika mwacilungamo ndithu (Masalmo 139:1-5; Miyambo 5:21).

Mulungu ndiye m’modzi, kulibe wina mulungu, koma ali yekha kukwaniritsa zofuna zonse za mitima yathu. Iye yekha Mulungu ayenera kuyamikidwa ndi kupembedzedwa (Deuteronomo 6:4). Mulungu ndi woulungama, kutanthauza kuti monga mwa cilungamo cace Mulungu sadzalekerera coipa. Ncifukwa ca cilungamo cace kuti ife tikakhululukidwe macimo, Yesu analandira mkwiyo wa Mulungu pamene macimo athu anatsikira pa Iye (Eksodo 9:27; Mateyu 27:45-46; Aroma 3:21-26).

Mulungu ndi wopambana, ndi woposa zonse. Ngakhale zonse zolengedwa zitaikidwa pamodzi sizikhoza kuposa colinga cace (Masalmo 93:1; 95:3; Yeremiya 23:20). Mulungu ndiye mzimu, kutanthauza kuti sapenyeka (Yohane 1:18; 4:24). Mulungu ali m’modzi mwa Atatu, kutanthauza kuti pakati pao, atatuwu ndi wofanana komanso olingana m’mphamvu, m’khalidwe ndi mu ulemelero. Taonani kuti ngakhale mau oyamba kuonapo anena za dzina lace kukhala limodzi osati ambiri, ngakhale kuti tinena za m’modzi mwa atatu – “Atate, Mwana, Mzimu Woyera” (Mateyu 28:19; Marko 1:9-11). Mulungu ndiye coonadi, kutanthauza kuti Iye abvomekeza m’mene aliri, ndipo Iye akhalabe wangwiro ndipo sanama ai (Masalmo 117:2; 1 Samueli 15:29).

Mulungu ndi woyera, ndipo ndiwopatulidwa pa kali konse dodetsedwa kapena coipa ciri conse. Mulungu aona coipa ndipo sakondwera ai. Mulungu amachulidwa kuti ndi moto wopsereza (Yesaya 6:3; Habakuku 1:13; Eksodo 3:2, 4-5; Ahebri 12:29). Mulungu ndi wacisomo, ndipo cisomo cace ciri ndi kukoma, cifundo ndi cikondi. Ngati sicinali cisomo cace Mulungu, ciyero cace cikadatipatula ife kwa Iye, sikudakakhala kotheka kuyanjana ndi Iye. Koma tiyamika popeza zinthu siziri tero ai, pakuti Iye afuna kutidziwa m’mene ife tiliri (Eksodo 34:6; Masalmo 31:19; 1 Petro 1:3; Yohane 3:16; 17:3).

Uku kwangokhala ngati kuyankha mwapafupi za funso limeneli lalikulu lonena za Mulungu. Conde khalani omasuka kumufunafuna Iye mu mtima mwanu nthawi zonse (Yeremiya 29:13).

EnglishBwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi makhalidwe a Mulungu ndi otani? Kodi Mulungu ali bwanji?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries