settings icon
share icon
Funso

Kodi tanthauzo la moyo nciani?” Kodi ndingapeze bwanji tanthauzo la moyo wanga?

Yankho


Kodi tanthauzo la moyo nciani? Kodi colinga, cisangalalo ndi zokhutitsa moyo zingapezeke bwanji? Kodi zinthu zosatha ndi zofunikira mu umoyo zingapezeke bwanji? Pali anathu ena amene akhala akulingalira pa mafunso oterewa mosalekeza. Ayangana kumbuyo mu zaka zao naona umo m’mene ubale wa umoyo wao unathera, motero kuti akhala ngati osowa pogwira, ngakhale kuti iwo anakwaniritsa cimene anali kufunitsitsa mu umoyo wao. Munthu wina wa masewera othamanga, atapambana pa masewera ace, tsiku lina wina anamufunsa iye, ngati panali munthu wina anamuuza kuthamanga pamene anayamba masewerawo. Wothamanga uja poyankha anati, “Ndikadakonda wina akadaniuza kuti ukadzafika pamwamba, pamenepo palibe kanthu kali konse.” Zinthu zambiri zimene zikhoza kupezedwa mu umoyo zimaonekera patsogolo pace kuti ndizopanda nchito ndithu.

Mu umuthu wathu, anathu amafuna zinthuzambiri ndipo amazilondola zimene zitenga mitima yao poganizira kuti mwa zimenezo adzapezamo zophindulitsa zabwino. Zina za zinthuzo ndi monga, nchito za mabizinesi, kukhala ndi cuma, ubale wabwino, zogonana, zokondweretsa thupi, ndi kukondweretsa ena powacitira zabwino. Anthu ena anena bwino kuti pamene iwo anakwaniritsa zofunazo mu umoyo wao monga kupeza cuma, kukhala ndi ubale wabwino kapena zina ziri zonse zimene anaziyesa zobweretsa cimwemwe, umoyo wao unakhalabe ngati wopanda kanthu mkati.

Wolemba buku la Mlaliki atiuza bwino za zimenezi pamene anena kuti,”Zacabecabe, ati Mlaliki; zacabecabe zonse ndi cabe” (Mlaliki 1:2). Mfumu Solomoni, amene analemba bukuli la Mlaliki, anali ndi cuma kwambiri, nzeru zambiri koposa anthu onse amene analiko pa nthawiyo ngakhale lero lino, anali ndi akazi mazana ambiri, nyumba ndi minda za ufumu zimene mafumu ena ankasilira, analinso ndi cakudya ndi vinyo wabwino kwambiri komanso iye anakondweretsedwa mw njira iri yonse imene anafuna pa nthawi yace. Iye anatero pa nthawi ina yake kuti ciri conse cimene mtima wace unafunitsitsa anacilondola nacipeza. Koma pano atsiliza motere “umoyo pansi padzuwa” – umoyo wokhala monga kuti zonse zokhuza umoyo wabwino ndi zinthu zopenyeka ndi maso kapena zimene tingazimve – umoyo ngwacabe. Ncifukwa ninji akutero, kuonetsa kuti palibe phindu? Cifukwa Mulungu anatilenga kuti tikaone zokoma koposa zopenyeka kapena zomveka pa umoyo. Ponena za Mulungu iye akutere, “Cinthu ciri conse anacikongoletsa pa mphindi yace; ndipo waika zamuyaya m'mitima yao ndipo palibe munthu angalondetse nchito Mulungu wazipanga ciyambire mpaka citsiriziro” (Mlaliki 3:11). Mu mitima mwathu tidziwa kuti “zapano-ndi-tsopano” si zonse zilipo pa umoyo wa munthu.

Mu Genesis, buku loyamba la mu Baibulo, m’menemo tipeza kuti Mulungu analenga munthu m’cifaniziro cake (Genesis 1:26). Ici cionetsa bwino kuti tili ngati Mulungu koposa cinthu cina ciriconse kapena mtundu wina uli wonse wa zolengedwa. Tiona kuti pamene munthu asanacimwe ndiponsi pamene tembelero lisanabwere padziko lapansi, zinthu izi zinali zoonadi: 1) Mulungu analenga munthu kukhala woyanjana ndi wina (Genesis 2:18-25); 3) Mulungu nali m’ciyanjano ndi munthu (Genesis 3:8); ndipo 4) Mulungu anamupatsa munthu mphamvu pa zolengedwa zina zonse (Genesis 1:26). Kodi cacikulu pa zonsezi ndi ciani? Mulungu anafuna kuti zonsezi zitithandize pa umoyo wathu ndi kukhala ndi moyo wacisangalalo, koma zonsezi (makamaka munthu kukhala pa ciyanjano ndi Mulungu) zinaonongeka kotheratu pamene munthu anagwa mu ucimo ndipo tembelero linalowa ndithu (Genesis 3).

Mu Chibvumbulutso, buku lothera mu Baibulo, Mulungu anena kuti adzaononga dziko lino ndi m’mwamba ndi kuikako cilengedwe ca tsopano, adzalenga m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano. Panthawi imeneyi adzabwezera zinthu kukhala pakale pa nthawi imene anangozilenga, ndipo adzakhazikitsa ubale ndi munthu woomboledwa ndipo iwo wosawomboledwa adzaweruzidwa ndi kupnyedwa mu Nyanja ya moto (Chibvumbulutso 20:11-15). Tembelero la cimo lidzacotsedwa, ndipo sipadzakhalanso cimo, cisoni, matenda, imfa, kapena cowawa (Chibvumbulutso 21:4). Mulungu adzakhala ndi iwo, ndipo iwo adzakhala ana ace (Chibvumbulutso 21:7). Potero zonse zidzakwaniritsidwa: Mulungu anatilenga kuti tikakhale m’ciyanjano ndi Iye, koma munthu anacimwa, naononga ciyanjanoco, ndipo Mulungu adzabwezeranso pakale ciyanjanoco mwathunthu. Inde munthu kupata zonse zofuna umoyo wace koma kufa kopanda Yesu ndiko kuti iye wazicotsa pamaso pa Mulungu nataya moyo wace wamtsogolo, umene uli moyo wosatha. Koma Mulungu wapereka njira kupyolera mwa kukhulupirira Yesu wopacikidwa pamtanda, kuti umoyo wosatha ulipo ndipo upezeka mwa Iye (Luka 23:43) komanso umoyo wapadziko umene uli wakoma ndi wophindulitsa. Kodi umoyo umenewu wabwino ndi wophindulitsa upezedwa bwanji?

Colinga ca umoyo cinakwaniritsidwa mwa Yesu Kristu

Colinga ceniceni mu umoyo, tsopano ndi mtsogolo, cipezeka cabe mukukwaniritsidwa kwa ubale ndi Mulungu, inde ubale umene unaonongeka pamene Adam ndi Hava anagwa mu ucimo. Ubale umenewo ndi Mulungu utheka cabe kupyolera mwa Mwana wace, Yesu Kristu (Macitidwe 4:12; Yohane 1:12; 14:6). Moyo wosatha umenewu umapezedwa tikalapa macimo athu (kulekelatu, osati kulingalira kuwacitanso mtsogolo) ndipo Kristu atisintha us, kutikonza kukhala cilengedwe catsopano ndipo tikhala odalira pa Yesu Krsistu ngati Mpulumutsi wathu.

Colinga ceniceni mu umoyo sicipezeka pobvomereza Yesu kukhala cabe ngati Mpulumutsi ai. Koma, Colinga ceniceni ca umoyo ndi pamene wina ayamba kulondola Kristu, kuphunzira za Iye, kukhala ndi Iye, kukhala mu Mau ace, kulumikizana ndi Iye mukupemphera, ndi kuyenda ndi Iye mwakumvera malamulo ace. Ngati sindiwe Mkristu, (kapena mwina wokhulupirira watsopano), mwina mukhoza kumanena izi kwa inu nokha, “Zimenezo sizioneka ngati zokondweretsa komanso ngati zaphindu kwa ine!” Koma Yesu ananena mau awa:

“Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani gori langa, ndipo phunzirani kwa Ine; cifukwa ndiri wofatsa ndi wodzicepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti gori langa liri lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka” (Mateyu 11:28-30). “Siikudza mbala, koma kuti ikabe, ndi kupha, ndi kuononga, Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nao wocuruka” (Yohane 10:10). “Pomwepo Yesu anati kwa ophunzira ace, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wace, nanditsate Ine. Pakuti iye amene afuna kupulumutsa moyo wace adzautaya: koma iye amene ataya moyo wace cifukwa ca Ine, adzaupeza” (Mateyu 16:24-25). “Udzikondweretsenso mwa Yehova; Ndipo iye adzakupatsa zokhumba mtima wako” (Masalmo 37:4).

Cimene mavesi onsewa akunena pano ndicakuti tili ndi umwai wopanga cisankho. Tikhoza kusankha kupitiliza kutsogolera miyoyo yathu, ndi kukhala wosakhutitsidwa, kapena titha kusankha kulondola Mulungu ndi kukhala ndi umoyo wokhutitsidwa cifukwa cakuti Iye ndiye adzatitsogolera ndi kutipatsa zonse zofunikira za umoyo motero tidzakutitsidwa. Izi ziri tero cifukwa cakuti Mlengi wathu atikonda ife ndipo atifunira zabwino zonse (koma osati umoyo wapafupi kapena wa see nthawi zonse, koma wakukhala ndi colinga).

Umoyo wa Ukristu tingaulinganize ndi munthu amene afuna kusankha m’mene adzaonerera bola (mpila), kuti kodi agule tiketi yodula yomulola iye kukhala pa mpando wapafupi kuti aone bwino, kapena agule tiketi ya mtengo wotsika ndi kuonerera bola patali. Kuonerera Mulungu akugwira nchito yace pafupi ndiye cinthu cofunikira kusankha, koma mwacisoni, kuti nthawi zambiri anthu sacita cisankho cotero. Kuonerera Mulungu akucita nchito yace ndi cinthu cokomera iwo olimbika mtima kutsata Kristu, iwo amene abvomerezadi kusiya zonse ndi kutsata cifuniro ca Mulungu mu umoyo wao. Alipila kale ndalama (pafunika kuzipereka kotheratu kwa Yesu kuti acite cifuniro cace); akukhala ndi umoyo wofikapo; ndipo akhoza kuziona iwo okha, munthu mzao, ndi Mlengi wao koma mosasamalira konse. Kodi mwalipira kale? Kodi mufuna kutero? Ngati ndi tero simudzakhala munthu wakukhal ndi njala yofunafuna zacabe.

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi tanthauzo la moyo nciani?” Kodi ndingapeze bwanji tanthauzo la moyo wanga?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries