settings icon
share icon
Funso

Kodi Baibulo linena ciani za mcitidwe wokonda zogonana wa pakati pa akazi kapena amuna okhaokha? Kodi mcitidwe wokonda zogonana wa pakati pa akazi kapena amuna okhaokha ndi cimo?

Yankho


Mobwerezabwereza, Bibulo litiuza kuti mcitidwe wokonda zogonana wa pakati pa akazi kapena amuna okhaokha ndi cimo (Genesis 19:1-13; Levitiko 18:22; Aroma 1:26-27; 1 Akorinto 6:9). Pa Aroma 1:26-27 aphunzitsa kuti mcitidwe wokonda zogonana wa pakati pa akazi kapena amuna okhaokha umadza cifukwa ca kukana ndi kumvera Mulungu. Pamene anthu asankha kupitiliza kukhala mu ucimo ndi kusakhulupirira, Mulungu “awapereka ku zofuna zao” zoipitsitsa kuti iwo aone kuipa kwa tsogolo lotero komanso kuipa kwa kusamvera Mulungu. Pa 1 Akorinto 6:9 pali mau akuti onse “oipa” sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.

Mulungu salenga munthu wolakalaka kapena wofunafuna mcitidwe wokonda zogonana wa pakati pa akazi kapena amuna okhaokha. Baibulo litiuza kuti anthu amatha kukhala tero kapena kucita zinthu zotero cifukwa ca ucimo (Aroma 1:24-27) komanso cifukwa ca zofuna zao. Munthu atha kubadwa wofuna za mcitidwe wokonda zogonana wa pakati pa akazi kapena amuna okhaokha, monganso momwe anthu ena amakhala wofuna kucita za ndeu ndi macimo ena. Zimenezo sizipereka cilolezo kuti munthuyo acimwe ai pocita mwa zofuna za mtima wace. Kodi ngati munthu abadwa ali ndi zilakolako zoipa zotero kodi pamenepo amapatsidwa mphamvu ya kucita zimenezo m’mene iye afunira? Ai! Zomemwezo ndi zoonanso tikafika pa nkhani ya mcitidwe wokonda zogonana wa pakati pa akazi kapena amuna okhaokha.

Ngakhale kuti ziri tero, Baibulo silinena kuti “mcitidwe wokonda zogonana wa pakati pa akazi kapena amuna okhaokha” ndi cimo “lalikulu” kuposa ena ai. Macimo onse ndi oipa kwa Mulungu. Mcitidwe wokonda zogonana wa pakati pa akazi kapena amuna okhaokha ndi m’modzi mwa zinthu zochulidwa pa 1 Akorinto 6:9-19 zimene zidzaletsa munthu kulowa mu ufumu wakumwamba. Monga mwa Baibulo, cikhululukiro ca Mulungu cilipo mosavuta monga momwe zadama zilipo mosavutanso kwa wocita dama, wopembedza mafano, wakupha kapena mbala (kawalala). Mulungu alonjeza kupereka mphamvu ya cigonjetso ca macimo, kuikapo macimo monga mcitidwe wokonda zogonana wa pakati pa akazi kapena amuna okhaokha, kwa iwo onse amene adzakhulupirira Yesu Kristu pa cipulumutso cao (1 Akorinto 6:11; 2 Akorinto 5:17; Afilipi 4:13).

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi Baibulo linena ciani za mcitidwe wokonda zogonana wa pakati pa akazi kapena amuna okhaokha? Kodi mcitidwe wokonda zogonana wa pakati pa akazi kapena amuna okhaokha ndi cimo?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries