settings icon
share icon
Funso

Kodi Baibulo linena ciani za madainasosi? Kodi madainasosi alimo mu Baibulo?

Yankho


Nkani ya nyama zodziwika kuti madainasosi mu Baibulo lakhala likukambidwa pakati pa Akristu kwa zaka zambiri, ndi colinga coti apeze kuti akhoza bwanji kumasulira bwino buku la Genesis, ndi momwe anagonere ndi kumasulira bwino umboni wooneka ndi maso umene ulipo. Pali magaulu awiri, ena aiwo aona dziko kukhala lakalekale ndipo akana motheratu kuti mu Baibulo sachulamo za madainasosi cifukwa, mwa kuganiza kwao, madainasosi anafa kalekale kwambiri zaka miyanda-miyanda zapitazo anthu asanalengedwe. Motero anthu amene analemba Baibulo sanazione nyama zimenezi mu moyo wao.

Iwo okhulupirira m’dziko losakhala lakalekale amakhala ndi cikhulupiriro cakuti ndizoona Baibulo linena za nyama zimenezi zochedwa madainasosi ngakhale kuti Baibulo siligwiritsa nchito liu lakuti “dainasosi.” Koma limagwiritsa nchito liu la mucihebri la tanniyn limene maBaibulo ena amalisanduliza kuti “cilombo cacikulu ca m’madzi” ndipo nthawi zina angonena kuti “njoka.” Koma ambiri amasanduliza liu limenelo kuti “cilombo cokhala ngati mng’azi” (diragoni). Ndipo tanniyn cioneka kuti cinalidi cilombo cacikuru kwambiri. Ndipo zirombo zimenezi zichulidwa mu Baibulo mu Cipangano Cakale, kwa makhumi asanu, ndipo zirombi zimenezi zinali kupezeka pamtunda komanso mu madzi.

Kuika nyama zikuluzikulu zochulidwa zokhala ndi mamba, Baibulo lifotokozera za zina mwa zolengedwazo motero kuti anthu ena amaphunziro akhulupirira kuti olembawo amanena za ma dinososi. Nyama yochedwa mvuu ndiyo imene aikhulupirira kuti inali yamphamvu kwambiri kuposa zolengedwa zina ziri zonse zapa dziko, ndipo mcira wace uyerekezedwa ndi mtengo wa mkungudza wochulidwa pa (Yobu 40:15). Ena mwa ophunzirawo ayesetsa kuti adziwe za nyama imeneyi ndipo pali maganizo ena akuganizira kuti ndi njobvu ndipo ena akuti ndi mvuu. Ndipo ena poganizirapo anenanso kuti ai, njovu ndi mvuu ziri ndi micira ing’ono-ing’ono motero sizingakhale nyama za mcira monga mwa mau apa Yobu 40:15 – kulinganiza kutalika kwa mcira monga mtengo wa mkungudza. Madinasosi awa analidi akuluakulu, okhala ndi micira yaikulu yolingana ndi kutalika kwa mtengo wa.

Pa kusintha kulikonse kwa masiku akalekale mumbiri ya dziko, amanenamo za nyama zina zazikuluzikulu zokhala ndi mamba. Zinthu zolembedwa pa miyala, zinthu zakale zoonetsa umoyo ndi zina zake zoumba-umba zimene zinapezeka ku dziko la kumpoto kwa America (North America) zioneka zofanana ndi madainasosi. Palinso nkhani zambiri zonena za nyama zotere komanso pali zina zooneka ndi maso pakati pa anthu ena makamaka mzigawo za kumpoto kwa dziko la Amerika komanso mzigawo zina za ku Asiya makamaka capakati koma kum’mwera pango’no kwa Asiya.

Ndiye pano funso ndilakuti, kodi madainososi alimo mu Baibulo? Nkhani imeneyi siyapafupi kuikhazikitsa kapena kuithetsa. Nkhani yonse igona pa m’mene munthu amvetsera ndi kumasulira umboni umene ulipo ndi m’mene munthu aonera malo omuzungulira. Ngati Baibulo limasuliridwa mwa mau mosasintha cina ciriconse, tidzamasulira kuona dziko lapansi ngati locepa ndi kubweretsamo maganizo akuti anthu ndi nyama zodziwika kuti dainososi zinali kukhala pamodzi ndi anthu. Ndipo ngati madainasosi ndi anthu anali kukhala pamodzi nanga cinacitika ndi ciani kuli madainasosi? Baibulo silinena za nkhani iyi, nyamazi mwina zinafa munthawi ya kutha kwa cigumula cifukwa ca kusintha kwa malo komanso cifukwa cina ndicakuti nyamazi zimasakidwa mosatha ndi anthu motero zinafa zonse.

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi Baibulo linena ciani za madainasosi? Kodi madainasosi alimo mu Baibulo?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries