settings icon
share icon
Funso

Ndingakhale bwanji bwino ndi Mulungu?

Yankho


Kukhala “bwino” ndi Mulungu, coyamba tiyenera ife kumvetsa kuti “coipa” nciani? Yankho ndi lakuti coipa ndi ucimo. “Anapatuka onse; pamodzi anabvunda mtima; Palibe wakucita bwino ndi mmodzi yense” (Masalmo 14:3). Talimbana ndi kumphwanya Malamulo a Mulungu; ndipo ife “tili ngati nkhosa zotaika” (Yesaya 53:6).

Coipapo pamenepa ndi cakuti cilango ca cimo ndi imfa. “Taonani …moyo wocimwawo ndiwo udzafa” (Ezekieli 18:4). Ndipo nkhani yabwino ndi yakuti Mulungu potikonda ife anakonza njira ya cipulumutso kuti ife tikapulumutsidwe. Yesu ananena bwino za cifuniro cimeneci pamene anati, “akuti Mwana wa munthu anadza kufunafuna ndi kupulumutsa, cotayikaco” (Luka 19:10), ndipo Iye anaonetsa kufikiritsidwa kwa cifuniro pamene anafa pa mtanda nanena mau awa, “Kwatha!” (Yohane 19:30).

Kukhala ndi ubale wabwino ndi Mulungu kumayamba ndi kubvomereza kwa macimo ake munthu. Cotsatapo, iye azicepetse nazipereke kwa Mulungu ndi kuulula macimo ace (Yesaya 57:15) nacite zones zothekera kusiya macimo amenewo kapena cimo limenelo. “Pakuti ndi mtima munthu akhulupira kutengapo cilungamo; ndi m'kamwa abvomereza kutengapo cipulumutso” (Aroma 10:10).

Kulapa kuyenera kukwaniritsidwa ndi cikhulupiriro – makamaka pokhulupira kuti Yesu anazipereka kukhala nsembe ya cipulumutso cathu ndikuti Iyeyo anauka kwa akufa ndipo ndiye Mpulumutsi. “kuti ngati udzabvomereza m'kamwa mwako Yesu ndiye Ambuye, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka” (Aroma 10:9). Pali mau ena ambiri amene anena za kufunikira kwa cikhulupiriro monga pa Yohane 20:27; Macitidwe 16:31; Agalatiya 2:16; 3:11, 26; ndi Aefeso 2:8.

Kukhala bwino ndi Mulungu kuli pakuyankhapo pa cymene Mulungu wakucitira m’malo mwako. Mulungu anatumiza Mpulumutsi, anapereka nsembe (Yesu Kristu) kukucotsera cimo lako (Yohane 1:29), ndipo aperekanso lonjezo “Ndipo kudzali, kuti yense amene akaitana pa dzina la Ambuye adzapulumutsidwa” (Macitidwe 2:21).

Nkhani yabwino kwambiri yokhuzana ndi kugonja ndi cikhululukiro ndi nkhani ya mwana wolowerera (Luka 15:11-32). Mwana wam’ng’ono uja anaononga cuma ca atate wace mwa njira yoipa, njira yaucimo (vesi 13). Pamene anazindikira kulakwa kwace, anaganizira zobwerera kunyumba ya atate wace (vesi 18). Iye anaganiza kuti sadzayesedwanso ngati mwana wapakhomopo (vesi 19), koma sizinali tero, anaphonya m’maganizo. Atate wace anakondetsetsa iye monga kale lonse (vesi 20). Iwo anamukhululukira zones ndipo, analamula kuti amucitire phwando (vesi 24). Mulungu ndiwabwino, Iye amasunga malonjezo ake onse, kuikapo lonjezo la kukhululukira. “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, Apulumutsa iwo a mzimu wolapadi” (Masalmo 34:18).

Ngati mufuna kukhala bwino ndi Mulungu, pano pali pemphero lapafupi. Kumbukirani kuti kunena pemphero limeneli kapena pemphero lina liri lonse sikudzakupulumutsani. Ndikukhulupirira mwa Yesu kokha kumene kudzakupulumutsani ku macimo. Pemphero imeneyi ndi njira cabe yakuonetsa cikhulupiriro cano kwa Mulungu ndi kumuyamika Iye pa cipulumutso canu. “Mulungu, ndidziwa kuti ndakucimwirani ndipo ndiyenera cilango cosatha. Koma Yesu Kristu anatenga cilango cimeneco m’malo mwa ine ndipo mwa Iye yekha ndikhululukidwa macimo anga onse. Ndaika cikhulupiriro canga ndi cipulumutso canga mwa Inu. Zikomo cifukwa ca cisomo canu ndi cikhululukiro ca macimo – cimene ciri mphatso ya moyo wosatha. Amen!”

Kodi mwapanga ganizo la Khristu chifukwa cha zimene mwawerenga pano? Ngati ndi choncho, chonde sindikizani batani la “Ndavomera kulandira Khristu lero” pansipa.

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Ndingakhale bwanji bwino ndi Mulungu?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries