settings icon
share icon
Funso

Kodi Mulungu ndi oona? Kodi ndingadziwe bwanji kuti Mulungu ndi oona?

Yankho


Tidziwa kuti Mulungu ndi oona cifukwa anadzionetsera Yekha kwa ife mwa njira zitatu: m’cilengedwe, mu Mau ace, ndi mwa Mwana wace, Yesu Kristu.

Cinthu coonetsa mosasutsana konse kuti Mulungu aliko, ndi zinthu zimene Iye anazipanga ndi kuzilenga. “Pakuti cilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zace ndizo mphamvu yace yosatha ndi umulungu wace; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mau akuwiringula” (Aroma 1:20). “Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; Ndipo thambo lionetsa nchito ya manja ace” (Masalmo 19:1).

Ngati munali ndi koloko yapadzanja pakati pa munda, simudzakhala ndi ciganizo cakuti yangopezeka pomwepo mwa ngo kapena kuti kucokera paciyambi inali pomwepo ai. Mukaionetsetsa mudzaona kuti pa dzina kapena liri ndi maonekedwe akuti inapangidwa. Koma pali wamkuru wopitilira akatswiri onse odziwa kupanga zinthu. Kapimidwe kathu ka nthawi sikadalira pa koloko yapadzanja, koma pa nchito yamanja ya Mulungu – kuzungulira kwa dziko ndi zina zosatha kuzifotokoza molingana ndi nzeru za munthu. Dziko ndi zolengedwa zace lionetsa kuti Mulungu ndi Mlengi wambambande ndithu.

Ngati mwapeza uthenga umene ufunikira kumasulidwa, mudzacita zothekera zonse kumasula kuti mudziwe za uthengawo. Mu mtima mwanu mudzafuna kudziwa kuti watumiza nkhani, iye amene analemba uthengawo. Mukaonetsetsa pa ukatswiri wace, m’maso mwathu anthufe zolengedwa zina zioneka zofana koma mukagang’ana kwambiri mudzaona kuti pali kusiyana, mwacitsanzo, taona mizere ya zala za kumanja kwa munthu, palibe and ndi mizere yolingana ndi wina, mukonanso, mudzaona monga kuti zomera zina zifanana koma sizifanana konse.

Mulungu sanapange dziko kukhala lokoma cabe ai, koma anaikamonso zonse zokondweretsa umoyo wa cilengedwe cake (Mlaliki 3:11). Munthu amvetsa ndi kudziwa kuti pali zambiri zinthu koposa zimene zioneka ndi maso. Kumvetsa kwathu kwa tsogolo kapena umoyo wosatha kuli pa njira ziwiri izi: kupanga lamulo ndi kupembedza.

Cisintho cili conse cacitukuko mu mbiri ya umoyo ciri ndi malamulo ofunikira kwambiri a cikhalidwe, amene angakhale ofanana ndi zikhalidwe za anthu ena. Mwacitsanzo, cikondi cabwino ndi coyamikiridwa pa dziko lonse lapansi, pamene bodza liri lonse sililoledwa. Ici cikhala ngati cikhalidwe ca umunthu – kuonetsera coipa ndi cabwino – paonetsa za Wamkurukuru amene atithandiza ife kudziwa za cokoma ndi coipa kwa ife kapena kwa anthu ena.

Momwemonso, padziko lonse lapansi, anthu akhala akutsatira cipembedzo monga momwe iwo adziwira. Kupembedza kumeneku kungakhale kosiyana koma aliyense ali ndi cidziwitso kuti pali “mphamvu yakuya” ndipo anthu azindikira bwino za cimeneci. Kupembedza kwathu kwa Mulungu kuonetsa kuti Mulungu anatilenga ife, “mu cifaniziro cake” (Genesis 1:27).

Mulungu anadzionetsera kwa ife kupyolera mu Mau ake, Baibulo. M’malemba onse, muli cidziwikire kuti Mulungu alikodi (Genesis 1:1; Eksodo 3:14). Munthu akalemba za umoyo wace, sataya nthawi kuzionetsera ngati alikodi. Momwemo Mulungu satayanso nthawi kuonetsa kuti Iye aliko mu Buku lace. M’mene baibulo lionetsera kusintha kwa moyo, cilungamo cace, ndi zodabwitsa zopezeka m’Malemba ace ziyenera kutisendeza pafupi ndi Mau ace.

Njira yacitatu m’mene Mulungu anadzionetsera kwa ife ndi mwa Mwana wace, Yesu Kristu (Yohane 14:6-11). “Paciyambi panali Mau, ndipo Mau anali kwa Mulungu, ndipo Mau ndiye Mulungu. Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wace, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi cisomo ndi coonadi” (Yohane 1:1, 14; onaninso pa Akolose 2:9).

Mu umoyo wa Yesu, Iye anasunga zonse zokhuza lamulo la M’cipangano Cakale ndi kukwaniritsa zonse zimene aneneri ananena zokhuza Mesiya (Mateyu 5:17). Iye anacita nchito zambiri zacifundo zothandiza anthu nacita zodabwitsa zambiri zoonetsa coonadi cake ndi kuonetsa umulungu wace (Yohane 21:24-25). Ndipo, patapita masiku atatu atafa Iye, anauka kwa akufa, coonadi cimene anthu ambiri mbiri anacitira umboni (1 Akorinto 15:6). Mbiri imeneyi ionetsa umoyo wake wa umunthu padziko komanso citsimikizo ca Umulungu wace. Monga momwe mtumwi Paulo ananenera, “Pakuti ndidziwadi kuti kulibe kanthu ka izi kadambisikira; pakuti ici sicinacitika m'tseri” (Macitidwe 26:26).

Tidziwa kuti nthawi zonse pali anthu ena amaganizo okaika komanso ali ndi maganizo ao okhuzana ndi Mulungu koma adzawerenga umboni moyenera. Koma pali ena amene akhalabe otsutsa ngakhale patakhala umboni wokwanira (Masalmo 14:1). Zonsezi zikhuza cikhulupiriro (Ahebri 11:6).

EnglishBwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi Mulungu ndi oona? Kodi ndingadziwe bwanji kuti Mulungu ndi oona?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries