settings icon
share icon
Funso

Kodi ndingadziwe bwanji cifuniro ca Mulungu mu moyo wanga? Kodi Baibulo linena ciani pa zakudziwa cifuniro ca Mulungu?

Yankho


Ndikofunikira kwambiri kudziwa cifuniro ca Mulungu. Yesu anati abale ake enieni ndi iwo amene amacita cifuniro Atate: “Pakuti ali yense acita cifuniro ca Mulungu, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo, ndi amai” (Marko 3:35). Mu fanizo la ana amuna awiri, Yesu acenjeza ansembe akuru andi atsogoleri cifukwa cakulephera kucita cifuniro ca Mulungu, ndipo kunena molunjika, “…simunalapa pambuyo pace, kuti mumvere iye” (Mateyu 21:32). Cifuniro ca Mulungu ndiko kulapa macimo yathu ndi kukhulupira mwa Yesu Kristu. Ngati sitinapange ciganizo coyamba, kulapa macimo, ndiko kuti takana cifuniro ca Mulungu.

Pamene talandira Yesu ndi cikhulupiriro, timakhala ana ace a Mulungu (Yohane 1:12), ndipo Iye amafuna kutitsogolerabe ndithu kuti tiyende mnjira yace. (Masalmo 143:10). Mulungu sabisa cifuniro cace pamaso pathu ai, afuna kuti ticidziwe ndithu. Ndicodziwikiratu kuti Mulungu ameneyu watipatsa kale cilangizo mwa njira zambiri kulingana ndi Mau ace. Ife tiyenera, “M'zonse yamikani; pakuti ici ndi cifuniro ca Mulungu ca kwa inu, mwa Kristu Yesu” (1 Atesalonika 5:18). Tiyenera kucita nchito zabwino (1 Petro 2:15). Ndipo “Pakuti ici ndi cifuniro ca Mulungu, ciyeretso canu, kuti mudzipatule kudama” (1 Atesalonika 4:3).

Cifuniro ca Mulungu cimadziwika ndipo ndikotheka kutsimikiza za ico. Aroma 12:2 akuti, “Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire cimene ciri cifuno ca Mulungu, cabwino, ndi cokondweretsa, ndi cangwiro.” Mauwa atipatsa ife zofunikira kwambiri izi: mwana wa Mulungu amakana kukhala wa dziko lapansi motero iye amazipereka kuti Mzimu amusithe kuti akhale oyanjana ndi Mulungu. Popeza nzeru zace zikhala zatsopano monga mwa zimene Mulungu amafuna, tsopano iye adziwe cifuniro cangwiro ca Mulungu.

Pamene tifuna cifuniro cake ca Mulungu, tiyenera kuona ndi kutsimikiza mu mtima mwathu kuti cymene tifuna, sindico cymene Baibulo liletsa, tikatero tikangana ndi coonadi. Mwacitsanzo, Baibulo liletsa kuba, popeza Mulungu anakambapo kale momveka bwino pa nkhani iyi, tidziwa kuti sindiyenera cifuniro cace kuti ife tipembe kukhala mbava za banki – sitiyenera kupemphera pa zotero ai. Cinanso ndicakuti tiyenera kuona kuti cymene tipempha cidzapereka ulemerero kwa Mulungu ndi kutithandiza ife ndi ena kukula mu mzimu.

Nthawi zina kudziwa cifuniro ca Mulungu ndikovuta cifukwa pamafunikira kuleza mtima kapena kudekha. Ndipo monga mwa umunthu wathu, munthu amafuna-funa atadziwa cifuniro ca Mulungu pomwepo mosayembekezera, koma sizimakhala tero kwa Mulungu. Iye amationetsera cifuniro cake pa nthawi yake mokhuzana ndi cikhulupiriro cathu ca mwa Iye. Cofunikira kwambiri ndi cakuti, pamene tiyembekezera malangizo otsatira, tiyenera kupitilizabe kucita zabwino zimene tidziwa (Yakobo 4:17).

Kawirikawiri tifuna Mulungu kuti atipatse zocita – kogwira nchito, kumalo kokhala, munthu wokwatira, galimoto yogula, ndi zina zotero. Mulungu atilola ife kupanga zisankho ndipo ngati tikhala mwa Iye, adzatithandiza kuti tisagwe mu zisankho zoipa (onani pa Macitidwe 16:6-7).

Munthu tikamodziwa bwino, pamenepo pakhalanso mpata wopanga ubale wakuya ndipo timatha kudziwa zofuna zace. Mwacitsanzo, pali zambiri zimene mwina mwana wam’ng’ono angafune kukhumba akamayenda ndi atate ake, ndipo zina za izo sayesa kuzitenga kapena kuziikako nzeru ngakhale kuti panthawiyo mtima wace unazifunitsitsa cifukwa adziwa kuti, “atate wanga sadzandilola ine kutero.” Iye sadzafunsa atate wace nthawi zonse kuti amulangize pa zinthi zina zonse cifukwa adziwa cimene atate ace amafuna cifukwa awadziwa iye. Comweco, cifanana ndi momwe ife tikhalira ndi Atate wathu, Mulungu, pa ubale wathu ndi Iye. Ndipo tikamayenda ndi Ambuye, kumva mau ace ndi kudalira pa Mzimu, tipeza kuti tipatsidwa nzeru ya Yesu (1 Akorinto 2:16). Timudziwa Iye, ndipo potero tithandizika kudziwa cifuniro cace. Timapeza kuti malangizo ake ali pafupi ndithu. “Cilungamo ca wangwiro cimaongola njira yace; Koma woipa adzagwa ndi zoipa zace” (Miyambo 11:5).

Ngati tiyendadi ndi Ambuye ndipo tifunitsitsa cifuniro cake mu miyoyo yathu, Mulungu adzaika zofuna zace pa mitima yathu. Cacikulu ndikufuna cifuniro ca Mulungu, osati cifuniro cathu. “Udzikondweretsenso mwa Yehova; Ndipo iye adzakupatsa zokhumba mtima wako” (Masalmo 37:4).

EnglishBwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi ndingadziwe bwanji cifuniro ca Mulungu mu moyo wanga? Kodi Baibulo linena ciani pa zakudziwa cifuniro ca Mulungu?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries