settings icon
share icon
Funso

Kodi cisamaliro cosatha cipezeka mu Baibulo?

Yankho


Anthu akadziwa Yesu kukhala Mpulumutsi wao, iwo amabwera mu ubale ndi Mulungu umene umapereka cisamaliro cosatha. Pa Yuda 24 mau atere, “Ndipo kwa iye amene akhoza kukudikirani mungakhumudwe, ndi kukuimikani pamaso pa ulemerero wace opanda cirema m'kukondwera,” Mphamvu ya Mulungu imateteza munthu kuti asagwe kuti pamaso pa Mulungu Munthuyo akhale wolungamitsidwa pamene aima mu ulemerero wa Mulungu. Cisamaliro cathu cosatha cimadza cifukwa cakuti Mulungu atisunga, osati pamene ife tisunga cipulumutso cathu ai.

Ambuye Yesu Kristu anati, “Ndipo Ine ndizipatsa moyo wosatha; ndipo sizidzaonongeka ku nthawi yonse, ndipo palibe munthu adzazikwatula m'dzanja langa, Atate wanga, amene anandipatsa izo, ali wamkulu ndi onse; ndipo palibe wina angathe kuzikwatula m'dzanja la Atate” (Yohane 10:28-29). Yesu Kristu pamodzi ndi Mulungu Atate atigwira ife m’dzanja lao kuti tisatengedwe. Kodi adzatipatutsa ife m’dzanja la Mulungu Atate ndi Mwana wace, ndani?

Pa Aefeso 4:30, pali mau akunena kuti, “Munasindikizidwa cizindikilo mwa iye, kufikira tsiku la maomboledwe.” Ngati okhulupirira akadakhala kuti alibe cisamaliro cosatha, kusindikizidwa kwao sikukadakhala kofikira kufikira pa tsiku la kuwomboledwa kwao, koma cothera cabe pamene iwo acimwa kapena aonetsa usakhulupira. Yohane 3:15-16 atiuza kuti ali yense wokhulupirira mwa Yesu Kristu “adzakhala ndi moyo wosatha.” Ngaati munthu analonjezedwa moyo wosatha, koma wacotsedwa kwa iye, ndiko kuti umoyo umenewu siunali “wosatha” kucokera paciyambi. Ngati cisamaliro ca umoyo wosatha sicoonadi, malonjezano a muoyo wosatha, sakadalembedwa mu Baibulo cifukwa kutero kukadakhala kuphonya ndithu.

Cofunika kudziwa cacukulu ca cisamaliro cosatha ciri pa Aroma 8:38-39 “Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu ziripo, ngakhale zinthu zirinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale colengedwa cina ciri conse, sicingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi cikondi ca Mulungu, cimene ciri mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” Cisamaliro cathu cosatha cagona pa cikondi ca Mulungu kwa iwo woomboledwa. Cisamaliro cathu cosatha cinagulidwa ndi Kristu, colonjezedwa ndi Mulungu ndiponso cosindikizidwa kapena cophimbidwa ndi Mzimu Woyera.

EnglishBwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi cisamaliro cosatha cipezeka mu Baibulo?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries