settings icon
share icon
Funso

Kodi mpikisano wobecha (njuga, kasino, lotare, jakipoti ndi zina) ndi cimo? Kodi Baibulo linena ciani za mpikisano wobecha?

Yankho


Baibulo silinena kanthu pa nkhani yakubecha, kumenya njuga ndi njira zina zacidule zopezeramo ndalama mwapafupi. Koma Baibulo limaticenjeza kuti, tisakondetsetse ndalama (1 Timoteo 6:10; Ahebri 13:5). Mau a Mulungu atilangizanso kuti tiyenera kukhala kutali ndi maganizo akufunitsitsa “kulemera mofulumira” ngakhale kosagwira nchito ina iri yonse ndithu (Miyambo 13:11; 23:5; Mlaliki 5:10). Mpikisano wobecha wagona pa kukondetsetsa ndalama ndipo anthu amakokedwa cifukwa mipikisano imeneyi imapereka ziganizo zoti munthu adzakhala ndi ndalama zocuruka pa nthawi yocepa cabe ndiponso mosavutikirapo konse.

Kodi pali vuto lotani kucita mpikisano wobecha? Mpikisano wobecha monga njuga ndi zina zotere, ndi ovuta kulowapo cifukwa ngati zimacitidwa mwa apo ndi apo ndiko kuti kutero ndi kutaya ndalama koma sicinthu coipa ai. Anthu amataya ndalama zao pa zinthu zambiri zosiyanasiyana. Kutaya ndalama pocita mpikisano wobecha ndi cimodzimodzi ndi kutaya ndalama kupita kukaona sinema (mwa nthawi zambiri), kapena kudya zakudya zodula kwambiri kapena kugula cinthu copanda nchito. Koma ngakhale kuti coonadi ndi cakuti ndalama zionongedwa pa zinthu zina, sindiko kunena kuti mpikisano wobecha wayenerezedwa ai. Ndalama siziyenera kuonongedwa pacabe. Ndipo ndalama zopitilirapo ziyenera kusungidwa kuti zikagwire nchito mtsogolo, kapena kupatsidwa kuti zithandize pa nchito ya Ambuye, osati kungozilowetsa zonse mu mpikisano wobecha.

Baibulo silinena molunjikiza mpikisano wobecha, koma inena za zocitika zina zimene zimadalira pa “umwai” kapena “m’pata.” Mwacitsanzo, kucita maere kugwiritsidwa nchito mu buku la Levitiko kuti asankhe pakati pa mbuzi imene idzakhala ndi kuperekedwa ngati nsembe ndi mbuzi imene adzaitumiza kuthengo ansembe atacita mwambo. Yoswa anacita maere pogawira ana Aisrayeli malo okhalako monga mwa mabanja ao. Nehemiya nayenso anacita maere kuona kuti ndani adzakhala mkati mwa linga la Yerusalemu. Ophunzira naonso amacita maere kuona kuti ndani amene adzalowa pamalo pa Yudasi Iskariote. Pa Miyambo 16:33 akuti, “Maere aponyedwa pamfunga; Koma ndiye Yehova alongosola zonse.”

Kodi nanga Baibulo linena ciani pa za kasino ndi malotare? Makasino ndi njira ina ya zamalonda imene anthu amanyengedwa kuikamo ndalama kucita mpikisano ndipo ndalamazo zikhoza kuphindula zina kapena zikhozanso kudyedwa. Ndipo ku malo amenewo nthawi zina kumapezeka zakumwa monga mowa waulere kapena wamtengo wotsika ndipo akamamwa nacita mpikisano umenewo, ndipo iwo satha kupanga maganizo aneru bwinobwino. Zonse m’malo otero ndizokonzedwa bwino motero kuti ndalama zimangopita kuli eni ake a malonda amenewo mwina kucotsako zocepa cabe zimene ena amawina. Ngakhale kuti ena acita malonda a malo otere a lotare amanena kuti ndalama zao athandizira anthu osauka ndi ena kuti aphunzire, kafukufuku aonetsa kuti nthawi zambiri iwo amene amapita kukacita mpikisano womweo, iwo womwe aperewera zambiri pa moyo wao. Cowapereka komweko ndi “kufuna kulemera mofulumira” ndipo limeneli likhala yesero lalikuru kwa iwo motero amangozipereka kuti ayese mwai wao. Ndipo mwai wakuti iwo akhoza ku wina umakhala wocepa kwambiri, motero kuti m’malo mopita patsogolo ndi zimene anali nazo, amangobweretsa mavuto pa iwo ndi pa anthu ena.

Kodi ndalama za loto, njuga, kapena mpikisano wina uliwonse wotere zikhoza kukondweretsa Mulungu? Anthu ambiri amanena kuti akucita mpikisano womwewo kuti ndalama zimene adzapeza, adzazipereka kuti zikathandize ku mpingo. Ngakhale kuti cilingo cotere cikhaladi cabwino, coonadi ndicakuti ndi anthu ocepa cabe amene akawina amakumbukira kuti agwiritsenso ndalamazo pa nchito zothandiza mu mpingo. Kafukufuku aonetsa kuti ambiri a anthu amene anawinako lotare kapena jakipoti, gawo lao la za cuma limagwa kotheratu patangopita zaka zocepa cabe ndipo mwina akhala osaukirapo koposa kale pamene asanawine lotareyo kapena jakipoti imeneyo. Ndi ocepa cabe amene ndalama zao zina amazipereka kuti zikathandize anthu ena. Mulungu zafuna ndalama zathu kuti nchito yake icitike padziko. Miyambo 13:11 akuti, “Cuma colandiridwa mokangaza cidzacepa; Koma wokundika ndi dzanja adzaona zocuruka.” Mulungu ndiye mwini zonse ndipo amapereka zofunikira mpingo wake kuti nchito yake yakufalitsa uthenga wabwino ipitebe patsogolo. Kodi Mulungu akhoza kucitiridwa ulemu polandira ndalama zocokera mukugulitsa makhwala oledzeretsa, kapena ndalama zakuba mu banki? Ai, sacitiridwa ulemu ndipo sakondwera. Komanso Mulungu safuna ngakhale ndalama zimene “zinabedwa” kucokera kwa anthu osauka mwa cilingo coti wina alemere, zonsezo sakondwera nazo.

Pa 1 Timoteo 6:10 akuti, “Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo cikondi ca pa ndalama; cimene ena pocikhumba, anasocera, nataya cikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri.” Ahebri 13:5 anena kuti, “Mtima wanu ukhale wosakonda cuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.” Ndipo pa Mateyu 6:24 akuti, “Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa cuma.”

EnglishBwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi mpikisano wobecha (njuga, kasino, lotare, jakipoti ndi zina) ndi cimo? Kodi Baibulo linena ciani za mpikisano wobecha?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries