settings icon
share icon
Funso

Kodi Yesu atafa anali kuti asanaukitsidwe pa masiku atatu aja a pakati pa imfa yace ndi kuukitsidwa kwace?

Yankho


Pa 1 Petro 3:18-19 akuti, “Pakuti Kristunso adamva zowawa kamodzi, cifukwa ca macimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma woparsidwa moyo mumzimu; 19m'menemonso anapita, nalalikira mizimu inali m'ndende.” Mau akuti mzimu akunena za mzimu wa Kristu Yesu. Ayanitsa pakati pa thupi lace ndi mzimu wace, osati pakati pa thupi lace ndi Mzimu Woyera ai. Thupi la Yesu linafa koma mzimu wace unakhalabe ndi moyo.

Pa 1 Petro 3:18-22 anenapo mau olumikiza kuzunzika kwa Kristu (vesi 18) ndi ulemerereo wace (vesi 22). Ndi Petro yekhayo amenen anena mwatsatanetsatane za zimene zinacitika pakati pa magawo awiriwa (kuzunzdidwa ndi ulemerero wace). Ma Baibulo ena a mu Cingerezi, monga, KJV anena kuti, Yesu “analalikira” kwa mizimu ya m’ndende (vesi 19). Ngakhale zili tero, liu la Cigiriki logwiritsidwa nchito pomwepo, si liu limene limagwiritsidwa nchito kawirikawiri mu Cipangano Catsopano akamanena za kulalikira uthenga. Mauwo atanthauza kuti, “kufuula kapena kulengeza uthenga”; ndipo ma baibulo ena a mu Cingerezi asanduliza mauwo kuti, “kufalitsa uthenga.” Yesu anazunzidwa ndipo anafa pamtanda, thupi lace linafadi. Koma mzimu wace unakhalabe ndi moyo, ndipo anaupereka m’manja a mulungu Atate (Luka 23:46). Monga mwa mau a Petro, nthawi ina pakati pa imfa yace Yesu, ndi nthawi ya kuukitsidwa kwace, nthawi ina, Iye anafalitsa uthenga kwa “mizimu yokhala m’ndende.”

Mu Cipangano Catsopano, liu lakuti mizimu igwiritsidwa nchito kunena angelo kapena mademoni kapena mizimu yoipa, osati anthu ai. Pa 1 Petro 3:20 Petro anena za “miyoyo”. Komanso, palibe pena paliponse mu Baibulo pamene atiuza kuti Yesu anapita ku gehena. Pa Macitidwe 2:31 pali mau akuti, Iye anapita ku Hade, koma Hade sindiko ku gehena ai. Hade ndi mau onena za malo a okhalako akufa, kumalo kumene akufa ayembekezera kuukitsidwa. Chibvumbulutso 20:11-15 mu ma Baibulo ena anena momveka bwino pakati pa mauwa a Hade ndi Nyanja ya moto. Nyanja ya moto ndi malo okhalako cikhalire, malo kumene iwo osocera ataweruzidwa adzakhala komweko ku nthawi zonse, Hade ndi malo okhalako cabe poyembekezera kumene osocera ndi oyera mtima a mu Cipangano Cakale akhala poyembekezera.

Ambuye wathu anapereka mzimu wace kwa Atate, ndipo anafa imfa ya thupi, nalowa mu paradaizo (Luka 23:43). Ndipo pa nthawi imeneyo panthawi ya pakati pa kufa kwace ndi kuukitsidwa kwace, Yesu anapitanso kumalo kumene anapereka uthenga kwa mizimu ya anthu (mwina angelo opandukawo; taonani pa Yuda 1:6), anthu amenewa anayelekezedwa monga anthu amene analiko pa nthawi ya cigumula ca Nowa (1 Petro 3:20). Petro satiuza kuti ndi uthenga wotani kapena kuti unali ndi mau otani uthenga umene Yesu anapereka kwa mizimu yomangidwayi, koma pano tinga siunali uthenga wacipulumutso popeza angelo sayenera cipulumutso, iwo sangapulumutsidwe (Ahebri 2:6). Cioneka kuti ndi uthenga wa cigonjetso ca Satana ndi amithenga ace (1 Petro 3:22; Akolose 2:15). Pa Aefeso 4:8-10 naponso paoneka kuti pali mau otithandiza kuona cimene yesu ankacita pa nthawi ya kufa kwace ndi kuukitsidwa kwace. Tiona bwino Paulo akunena za Yesu Kristu koma pa mau ocokera pa Malsalmo 68:18, “Munakwera kumka kumwamba, munapita nao undende kuuyesa ndende; Munalandira zaufulu mwa anthu, Ngakhale mwa opikisana nanu, kuti Yehova Mulungu akakhale nao” (Aefeso 4:8). Cioneka kuti mauwa aonetsa kuti izi zinacitika mu paradizo, Yesu anasonkhanitsa iwo onse woomboledwa ndi kupita nao kumalo a umoyo wosatha kokhala muyayaya kumwamba.

Baibulo silifotokoza cimene Yesu anali kucita pa masiku a pakati pa imfa yace ndi kuuka kwace. Cimene tinganene, ngakhale kuti anatontholetsa iwo amene anafa woyera mitima ndi kuwapereka kumalo a umoyo wosatha, Iye analalikira za kupambana kwace pa angelo oukira amene ali m’ndende. Cimene tidziwa motsimikiza ndi cakuti Yesu sanali kupereka mpata waciwiri wa cipulumutso; tikafa tiyenera ciweruzo (Ahebri 9:27), palibe mpata waciwiri. Cinanso, Iye sanali kuzunzika ku gehena; nchito yace yacipulumutso idathera pa mtanda (Yohane 19:30).

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi Yesu atafa anali kuti asanaukitsidwe pa masiku atatu aja a pakati pa imfa yace ndi kuukitsidwa kwace?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries