settings icon
share icon
Funso

Kodi umulungu wa Yesu upezeka mu Baibulo?

Yankho


Kuonjezera pa zimene Yesu ananena za Iye yekha, ophunzira ace naonso anabvomereza za umulungu wace wa Krsitu. Iwo anatero kuti Yesu ali ndi ufulu wakukhululukira macimo – cinthu cimene Mulungu yekha amacita – cifukwa ndi Mulungu amene amakhumudwa ndi ucimo (Macitidwe 5:31; Akolose 3:13; Masalmo 130:4; Yeremiya 31:34). Molinganiza kwambiri ndi mau otherawa, Yesu ndiye yemwe “adzaweruza amoyo ndi akufa” (2 Timoteo 4:1). Thomas polirira kwa Yesu anati, “Ambuye wanga ndi Mulungu wanga!” (Yohane 20:28). Ndipo Paulo achula Yesu kuti, “Mulungu wopambana ndi Mpulumutsi” (Tito 2:13) ndipo anenetsa kuti Iye asanabwere ku dziko lapansi, analiko kale ngati “Mulungu” (Afilipi 2:5-8). Ndipo Mulungu Atate akutere kunena za Yesu, “Mpando wacifumu wanu, Mulungu, ufikira nthawi za nthawi” (Ahebri 1:8). Yohane akuti, “Paciyambi panali Mau, ndipo Mau anali kwa Mulungu, ndipo Mau [Yesu] ndiye Mulungu” (Yohane 1:1). Zitsanzo za mau amene aphunzitsa za umulungu wa Kristu ndi zambiri zimene tingathe kuonapo (onani pa Chibvumbulutso 1:17; 2:8; 22:13; 1 Akorinto 10:4; 1 Petro 2:6-8; Masalmo 18:2; 95:1; 1 Petro 5:4; Ahebri 13:20), ndipo ngakhale limodzi lokha la mavesi amenewa ndilokwanira kuonetsa poyera kuti olondola ace a Yesu amutenga iye kukhala Mulungu.

Yesu nayeso apatsidwa maina opezeka ndi YHWH (dzina la Mulungu lodziwika bwino) mu Cipangano Cakale. Dzina lopezeka mu Cipangano Cakale lakuti, “muwomboli” (Masalmo 130:7; Hoseya 13:14) ligwiritsidwanso nchito mu Cipangano Catsopano (Tito 2:13; Chibvumbulutso 5:9). Yesu achedwa Immanueli – “Mulungu ali nafe” – mu Mateyu 1. Mu buku la Zakariya 12:10, ndi YHWH (Mulungu) amene akuti, “ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza.” Koma mauwa mu Cipangango Catsopano alozera kwa Yesu ponena za kupacikidwa kwace (Yohane 19:37; Chibvumbulutso 1:7). Ngati YHWH (Mulungu) wopyozedwa (kulasidwa) ndi kuyanganidwa ndipo Yesu ndiye amene anapyozedwa ndi kuyanganidwa, ndiko kuti Yesu ndiye YHWH. Kunena za mau apa Yesaya 45:22-23 Paulo akuti, mauwa alozera kwa Yesu Kristu monga mau apa Afilipi 2:10-11. Mopitiliza, dzina la Yesu limagwiritsidwa nchito kapena kuchulidwa mu pemphero pamodzi ndi dzina la Mulungu, “Chisomo ndi mtendere kwa inu zocokera kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Kristu” (Agalaatiya 1:3; Aefeso 1:2). Ngati Yesu si ndiye Mulungu ndiko kuti kutero ndi cimo la mwano woopsya. Dzina la Yesu lionekeranso pamodzi ndi dzina la Mulungu pamene analamulira iwo okhulupirira abatizidwe “mdzina (osati m’maina ai) la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera” Mateyu 28:19; komanso onani pa 2 Akorinto 13:14).

Zinthu zimene zitheka cabe ndi Mulungu zinaonekera ndi kucitidwa mwa Yesu. Yesu sanaukitse cabe akufa (Yohane 5:21; 11:38-44) ndi kukhululukira macimo (Macitidwe 5:31; 13:38), Iye analenga dziko ndipo alisunga (Yohane 1:2; Akolose 1:16-17). Ici cimveka bwino pamene wina aganizira za mau akuti YHWH (Mulungu) akuti Iye anali yekha pacilengedwe ca dziko (Yesaya 44:24). Tikaonanso bwino, Kristu alinso ndi zimene Mulungu ali nazo zimene zipezeka cabe mwa umulungu wace: ndi wamuyaya (Yohane 8:58), ali ponse-ponse (Mateyu 18:20; 28:20), adziwa zonse (Mateyu 16:21), ndi wamphamvu yonse (Yohane 11:38-44).

Abale ndi cinthu cina kuyeselera kuti munthu ndi Mulungu kapena kupusika wina kuti akhulupirire kuti zimenezo ndi zoona ndi kupereka zizindikiro zotsimikizira coonadico. Kristu anaonetsa zizindikiro zodabwitsa zambiri kuonetsa umulungu wace. Zina mwa zodabwitsa zimene Yesu anacita ndi izi: kusandutsa madzi kukhala vinyo (Yohanse 2:7), Kuyenda pa madzi (Mateyu 14:25), kuculukitsa zinthu zooneka (Yohane 6:11), kuciritsa osaona (Yohane 9:7), kuciritsa olemala (Marko 2:3), ndi odwala (Mateyu 9:35; Marko 1:40-42), ndi kuukitsa ena mwa akufa (Yohane 11:43-44; Luka 7:11-15; Marko 5:35). Yesu amene, anauka kwa akufa. Mu mbiri yonse kulibe milungu imene imatero ai pakati pa iwo opembedza milunguyo palibe umboni wotero. Kuuka kwa Yesu ndikopambana ndi koposa ndithu popeza ngakhale Mau a Mulungu ananena za Iye kuti adzauka.

Pali Mfundo khumi ndi ziwiri zonena za mbiri ya Yesu zimene ngakhale okhunzira osakhulupira pa Cikristu atsimikizira ndi kubvomereza.

1. Yesu anafa popacikidwa pa mtanda.
2. Iye anaikidwa m’manda.
3. Imfa yace inadzetsa cisoni kwa ophunzira ndipo anataya ciyembekezo.
4. Manda ace anapezedwa (kapena anenedwa kuti anapezedwa) opanda kanthu mkati patangopita masiku ocepa.
5. Ophunzira anakhulupirira kuti anaona Yesu oukitsidwa kwa akuf.
6. Zitacitika izi, ophunzira analimbikitsidwa m’cikhulupiriro cao komanso analimbika mitima.
7. Uthenga uwu unakhala Mfundo lalikuru la kufalitsa uthenga pakati pa okhulupirira woyamba.
8. Uthenga uwu unalalikidwa mu Yerusalemu.
9. Ndiye cifukwa ca kulalikiridwa kwa uthenga uwu, mpingo unabadwa ndipo unakula.
10. Tsiku la kuuka kwake, la Sondo, linalowa m’malo mwa tsiku la Sabata (Ciweru) ngati tsiku la cipembedzo.
11. Yakobo, wokaika, anasinthika pamene nayenso anakhulupirira kuti anaona Yesu oukitsidwa.
12. Paulo, amene anali mdani wa Akristu, nayenso anasinthidwa atakumana ndi kukhulupirira Yesu oukitsidwayo mu umoyo wace.

Ngakhale kuti pali wina wotsutsana ndi mndandanda wopatsidwawo, pali ocepa cabe amene ayenera kutsimikiza za kuukitsidwa ndi uthenga wabwino: Imfa ya Yesu, kuikidwa kwace, ndi kuukitsidwa ndi kuonekeranso kwa anthu (1 Akorinto 15:1-5). Ngakhale kuti pangakhale njira zina m’mene ena atha kumasulira mfundo zina zopatsidwa pamwambapa, kuuka kwace kumangilira zonse pamodzi. Ngakhale otsutsa abvomereza kuti ophunzira ace anaona Yesu oukitsidwa. Palibe bodza liri lonse ngakhale mau ena amene akhoza kusintha zocitikazo za umboni wofikapo zokhuzana ndi kuuka kwa Yesu. Coyamba iwo akadaphindula ciani? Cikristu panthawiyo sicinali ponseponse ai ndipo sicinawapangile iwo ndalama. Caciwiri, anthu abodza satha kulola kuti afe pa cikhulupiriro cao. Palibe mau ena amene atha kumasulira kuti za comwe kuuka kwa Yesu kunacita mu miyoyo ya ophunzira, maka maka m’mene iwo analola kuzunzidwa ndi kuphedwa cifukwa ca cikhulupiriro cao pa Yesu. Inde, anthu ambiri amafa nayo bodza imene iwo aganiza kapena akhulupirira kuti ndiyoona, koma anthu sakufa pa zimene iwo adziwa kuti ndi zabodza.

Potsiliza, Kristu ananena kuti ndiye YHWH (Mulungu), kuti anali mulungu (osati cabe “mulungu” koma Mulungu m’modzi woona); omutsatira Iye (Ayuda amene akadaopa za kupembedza milungu ina) anamukhulupirira Iye namuchula Iye kuti ndi Mulungu. Kristu anaonetsera poyera umulungu wace pocita zizindikiro zodabwitsa kuikapo kuuka kwa akufa. Kulibe mau ena amene atha kumasulira bwino za ici koposa Iyeyo. Umulungu wace ndi oona ndithu umene Baibulo limasulira mwakuya.

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi umulungu wa Yesu upezeka mu Baibulo?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries