settings icon
share icon
Funso

Kuzithetsa nyere – Kodi ndi cimo monga mwa Baibulo?

Yankho


Baibulo silifotokoza poyera za mcitidwe wozithetsa nyere komanso silinena poyera kuti kutero ndi ucimo. Mau amene amaonedwa kwambiri pa nkhani iyi ndi mau a nkhani ya Onani opezeka pa Genesis 38:9-10. Ena amamasulira mau awa akuti “kutaya mbeu” pansi kukhala ngati cimo. Koma sicimene mau anena apa ai. Mulungu anamulanga Onani sicifukwa cakuti iye “anataya mbeu” koma cifukwa cakuti Onani anakana kucita nchito imene anamupatsa kuti mkaziyo (mlamu wace) akhale ndi mwana wa mkuru wace. Nkhani iyi siyakuzithetsa nyere pozigwira-gwira umalisece ai, ndi yakukana kucita nchito ya m’banja. Nkhani ina yaciwiri imene imagwiritsidwa nchito ponena za mcitidwe wotere wozigwira-gwira kumalo obisika kukhala ngati cimo ipezeka pa Mateyu 5:27-30. Yesu aletsa kukhala ndi maganizo a zilkolako zotero pamena akuti, “Ndipo ngati dzanja lako lamanja likulakwitsa iwe, ulidule, nulitaye.” Pano pali kusiyana pakati pa nkhani iyi ndi nkhani yoseweretsa umalisece kuzikondweretsa, ndipo cioneka kuti pano Yesu sanali kunena za nkhani yozigwira-gwira umalisece kuthetsa nyere.

Baibulo silinena poyera kuti mcitidwe wozithetsa nyere ndi cimo, palibe yankho yakuti kucita tero kapena zodzetsa zimenezo ndi cimo. Koma nthawi zonse mcitidwe umenewo ukhala wodzala ndi zilakolako, maganizo ofuna kutero, kuziutsira zilakolako zotero komanso mwina mwa kuona zithunzi-thunzi za umalisece wa ena.Ndi gwero limeneli la mavuto limene liyenera kuthetsedwa. Ngati macimo a zilakolako, maganizo oipa komanso kufuna kuona zithunzi-thunzi za umalisece zithetsedwa, ndiko kuti vuto lofuna kuthetsa nyere pozigwira-gwira lithetsedwa ndithu. Anthu ambiri amavutika mu umoyo wao pamene akumbukira zocita zao zotero pamene umwai wolapa ulipo.

Pali ziphunzitso zopezeka mu Mau a Mulungu zimene tiyenera kugwiritsa nchito pa nkhani iyi. Aefeso 5:3 akuti, “Koma dama ndi cidetso conse, kapena cisiriro, zisachulidwe ndi kuchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima kapena cinyanso.” Tikasunga mauwo, nkhani ya cilakolako siikhoza kuganiziridwa ai. Baibulo litiphunzitsa, “Cifukwa cace mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale mucita kanthu kena, citani zonse ku ulemerero wa Mulungu” (1 Akorinto 10:30). Ngati zocita sizipereka ulemelero kwa Mulungu, musacite zimenezo. Ngati munthu akaika kaika kuti cocita sicizakondweretsa Mulungu, ameneyo asacite cimene akuganizira. “Ndipo cinthu ciri conse cosaturuka m'cikhulupiriro, ndico ucimo” (Aroma 14:23). Tiyeneranso kukumbukira kuti matupi athu anaomboledwa ku ucimo ndipo tsopano ali ace a Mulungu. “Kapena simudziwa kuti thupi lanu liri kacisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha. Pakuti munagulidwa ndi mtengo wace wapatali; cifukwa cace lemekezani Mulungu m'thupi lanu” (1 Akorinto 6:19-20). Coonadi cimeneci ciri ndi zotuluka zace pa umoyo wathu. Ndipo monga mwa ziphunzitso izi, tiona kuti kuzigwira-gwira pofuna kuthetsa nyere ndi cimo ndithu. Ndicodziwikiratu kuti kutero sikupereka ulemelero kwa Mulungu; kutero ndi kuonetseratu ucimo ndi kukana kuti matupi athu ali ace a Mulungu.

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kuzithetsa nyere – Kodi ndi cimo monga mwa Baibulo?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries