settings icon
share icon
Funso

Kodi pemphero la munthu ocimwa nciani?

Yankho


Pemphero la munthu ocimwa ndilo pemphero limene munthu amapemphera kwa Mulungu akadziwa kuti ndi ocimwa ndipo ayenera kulandira Mpulumutsi. Kunena pemphero limeneli kokha sikuthandiza pa umoyo wa munthu. Pemphero la munthu ocimwa lenileni lionetsa cimene munthu adziwa, ndi kukhulupira za kuipa kwace kwa macimo motero kuti ayenera kulandira cipulumutso.

Gawo loyamba la pemphero la munthu ocimwa ndi kudziwa kuti ife tonse ndife ocimwa. Aroma 3:10 anena, “monga kwalembedwa, Palibe mmodzi wolungama, inde palibe mmodzi.” Baibulo linena bwino kuti ife tonse tinacimwa. Ife tonse ndife ocimwa amene tiyenera kulandira cifundo ndi cikhululukiro kucokera kwa Mulungu (Tito 3:5-7). Cifukwa ca ucimo wathu tiyenera kulandira cilango cosatha (Mateyu 25:46). Pemphero la munthu ocimwa ndiko kulira kupempha cifundo ca Mulungu ndi kupewa mkwiyo wace.

Gawo laciwiri la pemphero la munthu ocimwa ndi kudziwa cimene Mulungu anapereka pothetsa vuto ili. Mulungu anadza mwa umunthu ngati Yesu Kristu (Yohane 1:1, 14). Yesu anatiphunzitsa za coonadi ca Mulungu nakhala wolungama komanso wopanda cimo mu umoyo wake (Yohane 8:46; 2 Akorinto 5:21). Yesu anatifera ife pa mtanda m’malo mwathu, kutenga cilango cimene ife tikadalandira (Aroma 5:8). Yesu anauka kwa akufa kuonetsa cigonjetso pa ucimo, imfa ndi Gehena (Akolose 2:15; 1 Akorinto 15). Cifukwa ca zonsezi, macimo athu atha kukhululukidwa ndipo titha kulandira lonjezano la moyo wosatha wa Kumwamba – tikangoika cikhulupiriro cathu mwa Yesu Kristu. Ife tiyenera kukhulupirira kuti Iye anatifera ndipo anauka kwa akufa (Aroma 10:9-10). Titha kupulumutsidwa mwa cisomo cokha, mwa cikhulupiriro cokha, mwa Yesu yekhayo. Aefeso 2:8 akuti, “Pakuti muli opulumutsidwa ndi cisomo cakucita mwa cikhulupiriro, ndipo ici cosacokera kwa inu: ciri mphatso ya Mulungu.”

Kunena pemphero la ocimwa ndi kutsimikiza kwa Mulungu kuti udalira pa Yesu Kristu ngati Mpulumutsi wako. Kulibe mau ena amene ali obweretsa cipulumutso. Ndikukhulupirira cabe mwa Yesu, imfa yace ndi kuuka kwace kumene kutipulumutsa. Ngati umvetsa kuti ndiwe ocimwa ndiponso ufuna cipulumutso kupyolera mwa yesu Kristu, pali pemphero la ocimwa limene ungather kupemphera kwa Mulungu: “Mulungu ndidziwa kuti ndine ocimwa. Ndidziwa bwino kuti ndiyenera kulangidwa cifukwa ca zolakwa zanga. Koma ndikhulupira mwa Yesu Kristu kundipulumutsa. Ndikhulupirira kuti imfa yace ndi kuukitsidwa kwace kunabweretsa cikhululukiro pa ine. Ndikhulupira mwa Yesu, ndipo Yesu yekhayo ndiye Ambuye ndi Mpulumutsi wanga. Zikomo Ambuye, pondipulumutsa ndi kundikhululukira! Amen!”

Kodi mwapanga ganizo la Khristu chifukwa cha zimene mwawerenga pano? Ngati ndi choncho, chonde sindikizani batani la “Ndavomera kulandira Khristu lero” pansipa.

EnglishBwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi pemphero la munthu ocimwa nciani?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries