settings icon
share icon
Funso

Kodi Mzimu Woyera ndani?

Yankho


Pali kusamvetsa kwakukulu pa comwe Mzimu Woyera ali? Ena aona Mzimu Woyera kukhala ngati mphamvu yobisika yapadera. Ena amvetsa Mzimu Woyera kukhala ngati mphamvu yopatsidwa ndi Mulungu kwa iwo otsatira Yesu. Kodi Babulo linenapo ciani za kuzindikira kwa Mzimu Woyera? Mosataya nthawi, babulo likuta Mzimu Woyera ndiye Mulungu. Komanso Baibulo litiuzanso kuti Mzimu Woyera ndi umunthu wa Umulungu, munthu wokhala ndi maganizo, cifuno ndi cifuniro.

Mzimu Woyera ndiye Mulungu, izi zionekera mu Mau ake ambiri monga pa Macitidwe 5:3-4. Mu ndime iyi Petro anena ndi Hananiya cifukwa ninji Hananiya ananama kwa Mzimu Woyera ndipo mau akuti, “sunanyenga anthu, komatu Mulungu.” Apa ndizoonekeratu kuti kunamiza Mzimu Woyera ndiko kunamiza Mulungu. Tidziwanso kuti Mzimu Woyera ndiye Mulungu cifukwa Iye ali ndi zimene Mulungu ali nazo. Mwacitsanzo, Iye ali pali ponse monga tiona pa Masalmo 139:7-8, “Ndidzapita kuti kuzembera mzimu wanu? Kapena ndidzathawira kuti kuzembera nkhope yanu? Ndikakwera kumka kumwamba, muli komweko; Kapena ndikadziyalira ku Gehena, taonani, muli komweko.” Ndipo pa 1 Akorinto 2:10-11, tiona kuti Mzimu Woyera nayenso ali pali ponse “Koma kwa ife Mulungu anati onetsera izi mwa Mzimu; pakuti Mzimu asanthula zonse, zakuya za Mulungu zomwe. Pakuti ndani wa anthu adziwa za munthu, koma mzimu wa munthuyu uli mwa iye? Momwemonso za Mulungu palibe wina azidziwa, koma Mzimu wa Mulungu.”

Titha kudziwa kuti mwa Mzimu Woyera muli umunthu cifukwa Iye ali ndi nzeru kapena maganizo, ndi cifuno. Mzimu Woyera amaganiza ndipo adziwa (1 Akorinto 2:10). Mzimu Woyera agakwiitsidwe kapena kucitidwa cipongwe (Aefeso 4:30). Mzimu Woyera ndi mkala pakati kutipempherera (Aroma 8:26-27). Amapanga ziganizo monga mwa kufuna kwake. (1 Akorinto 12:7-11). Mzimu Woyera ndi Mulungu, kukhala ngati wacitatu mwa Mulungu M’modzi mwa Atatu (Mulungu Atate, Mwana ndi Mzimu Woyera). Ndipo ngati Mulungu Mzimu Woyera acita nchito ya kutonthoza ndi kulangiza ngati Nkhoswe amene Yesu analonjeza (Yohane 14:16, 26; 15:26).

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi Mzimu Woyera ndani?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries