settings icon
share icon
Funso

Kodi ubatizo wa Cikristu ndiwofunikira motani?

Yankho


Kwa Akristu, ubatizo ndi woikika ndi kukhazikitsidwa ndi Yesu Kristu umene Yesu analamulira mpingo kucita tero. Asanapite kumwamba, Yesu anati, “Cifukwa cace mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu; ndipo onani, Ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira cimariziro ca nthawi ya pansi pano” (Mateyu 28:19-20). Malamulo awa aonetsa kuti mpingo unapatsidwa mphamvu ndi udindo wakuphunzitsa mau a Yesu, kukopa ena kuti adziwe ndi kulondola Yesu, ndi kuwabatiza iwo. Zinthu izi ziyenera kucitika pali ponse (“ku maiko onse”) kufikira “cimariziro ca nthawi ya pansi pano.” Motero, kulibe cifukwa cina ai, ubatizo ndi wofunikira cifukwa unaikidwa ndi Yesu Kristu.

Ubatizo unali kucitika ngakhale pamene mpingo usanayambe. Ayuda kalero anali kubatiza iwo wolandiridwa kukhala ngati acipembedzo cimodzi ndipo ubatizo unaonetsa “kuyeretsedwa” kwao. Yohane M’batizi anagwiritsa nchito ubatizo kukonza njira ya Ambuye, imene aliyense, osati a Heleni okha, anayenera kulondola, kubatizika cifukwa aliyense afunika kulapa. Koma ubatizo wa Yohane wakulinga kukulapa siufanana ndi ubatizo wa Cikristu, monga tiona mu buku la Macitidwe 18:24–26 ndi 19:1–7. Ubatizo wa Cikristu uli ndi tanthauzo lakuya kwambiri.

Ubatizo uyenera kucitika m’dzina la Atate, Mwna ndi Mzimu – ici ndico cipangitsa kuti ubatizo umenewo uchedwe ubatizo wa “Cikristu.” Ndi cizindikiro cimeneci ca ubatizo coikidwa ndi Ambuye, munthu amaloledwa kukhala mu mpingo. Tikapulumutsidwa, “tibatizidwa” ndi Mzimu mthupi la Kristu, limene liri mpingo wace. Pa 1 Akorinto 12:13 pali mau awa, “Pakutinso mwa Mzimu mmodzi ife tonse rinabatizidwa kulowa m'thupi limodzi, ngakhale Ayuda, ngakhale Ahelene, ngakhale akapolo, ngakhale mfulu; ndipo tonse tinamwetsedwa Mzimu m’modzi.” Ubatizo wa madzi ndi cizindikiro ca ubatizo wa Mzimu.

Ubatizo wa Cikristu, ndiyo njira yokha imene munthu atha kuonetsa ku gulu la anthu kuti iyeyo ndi wokhulupirira komanso kuti wotsata Yesu. Mu ubatizo wa madzi munthu adzaonamo mau awa, “Ndionetsa cikhulupiro canga mwa Kristu; Yesu wandisambitsa ndi kuyeretsa moyo wanga ku macimo, ndipo tsopano ndiri ndi umoyo watsopano ndiponso ndine wopatulidwa.”

Ubatizo wa Cikristu uonetsa, imfa, kuikidwa m’manda, ndi kuukitsidwa kwa Kristu. Pa nthawi imodzinso uonetsa kuti tikufa ku macimo ndipo tilandira moyo watsopano mwa Kristu. Pamene wocimwa alapa ndi kuulula macimo ace kwa Amuye Yesu, iye amafa ku ucimo (Aroma 6:11) ndipo amaukitsidwa atalandira moyo watsopano (Akolose 2:12). Kumizidwa m’madzi kuonetsa kufa mu ucimo, ndipo kutuluka m’madzi kuonetsa kuyeretsedwa, moyo woyera umene umadza pambuyo pakupulumutsidwa. Pa Aroma 6:4 mau akutere: “Cifukwa cace tinaikidwa m'manda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo kulowa mu imfa; kuti monga Kristu anaukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, cotero ifenso tikayende m'moyo watsopano.”

Kunena mwa njira ina yapafupi, ubatizo ndico cizindikiro cabe cakubwalo cakuonetsa kusintha kwa mkati mwa mtima wa munthu atayamba kukhulupirira. Ubatizo wa Cikristu ndiko kumvera Ambuye munthu atalandira cipulumutso; ngakhale kuti ubatizo uyerekezedwa kukhala pafupi ndi cipulumutso, si uli cimodzi mwa zinthu zofunikira kuti munthu alandire cipulumutso. Baibulo imationetsa m’mavesi ambiri kuti mndandanda wake wa zinthuzi umacitika motere: 1) munthu akhulupirira mwa Ambuye Yesu ndipo 2) amabatizidwa. Zimenezi zionetsedwa pa Macitidwe 2:41, “Pamenepo iwo amene analandira mau ace anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu” (onaninso pa Macitidwe 16:14–15).

Wokhulupirira watsopano mwa Yesu Kristu ayenera afunitsitse kuti abatizidwe posacedwa. Mu Macitidwe 8, Filipo alankhula za “uthenga wabwino wa Yesu” kwa munthu wina wa ku Aitiopiya, mdindo wamphamvu wa Kandake, mfumu yaikazi ya Aaitiopiya, ndipo, iye akuti, “pamene anali kuyenda mnjira, anafika pamene panali madzi ndipo mdindo uja anati, ‘Taonani, pali madzi pano. Kodi cingaletse kuti ndi batizidwe ndi ciani?’” (mavesi 35-36). Pomwepo iwo aimitsa gareta uja, ndipo Filipo anabatiza munthu uja.

Ubatizo uonetsa kuti mkristu azindikira za imfa ya Yesu, kuikidwa ndi kuikanso kwa akufa. Kuli konse uthenga ukulalikidwa ndipo andthu akukokedwa ku cikhulupiriro ca mwa Kristu, motero ayenera iwo kubatizidwa.

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi ubatizo wa Cikristu ndiwofunikira motani?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries