settings icon
share icon
Funso

Ndingathe bwanji kugonjetsa cimo mu umoyo wanga wa CiKristu?

Yankho


Baibulo litipatsa magawo ambiri m’mene tingagonjetsere cimo. Mu umoyo wathu wapa dziko pano sikotheka kukhaliratu woyera ndi wopanda cimo (1 Yohane 1:8), koma tiyenera kuyesetsa ndithu kukhala wopanda cimo. Mwathandizo la Mulungu ndi kulondola ciphunzitso ca Mau ake, titha kugonjetsa cimo ndi kukhala monga Kristu.

Coyamba Baibulo linena za Mzimu Woyera amene akhala woyamba kutithandiza kugonjetsa cimo. Mulungu atipatsa Mzimu Woyera kuti tikhale wopambana mu umoyo wathu ngati a Kristu. Mulungu aonetsa kusiyana pakati pa nchito za thupi ndi cipatso ca Mzimu mu Agalatiya 5:16-25. Mu ndime zimenezo Mau afuna kuti tiyende mu Mzimu. Okhulupirira onse ali ndi Mzimu WOyera, koma mau awa atiuza kuti tiyende mu Mzimu, kumvera cimene Iye anena kwa ife pamene tiyenda. Ici citanthauza kusankha kulondolabe Mzimu Woyera mu umoyo wathu onse osati kulondola zafuna za thupi.

Kusiyana kumene Mzimu Woyera atha kucita mu umoyo wa munthu kuonekera mu umoyo wa Petro, amene, asanadzadzidwe ndi Mzimu Woyera, anakana Yesu Kristu katatu – pambuyo ponena kuti adzalondola ndi kufa naye limodzi. Atadzadzidwa ndi Mzimu Woyera, iye analankhula poyera komanso molimbika pakati pa Ayuda pa tsiku lija la Pentecoste.

Tiyenda mu Mzimu pamene sitizima cifuniro ca Mzimu (monga mwa 1 Atesolonika 5:19) ndi kufuna kudzadzidwa ndi mzimu (Aefeso 5:18-21). Kodi munthu amadzadzidwa bwanji ndi Mzimu Woyera? Choyamba, ndi Mulungu amene amasankha, monga m’mene zimacitikira mu Chipangano Cakale. Anasankha wina kucita ndi kutsiliza nchito imene inalipo ndipo anawadzadza ndi Mzimu (Genesis 41:38; Eksodo 31:3; Numeri 24:2; 1 Samueli 10:10). Pali umboni wokwanira pa Aefeso 5:18-21 ndi Akolose 3:16 ndipo Mulungu asankha kudzadza iwo amene amakhala mu Mau ake a Mulungu. Ici citipeleka ku gawo laciwiri.

Mau a Mulungu, Baibulo, linena kuti Mulungu watipatsa Mau ake kutithandiza ife pa nchito ina iri yonse (2 Timoteo 3:16-17). Litiphunzitsa ife mokhalira komanso comwe tiyenera kukhulupirira, tikasankha njira yoipa, Baibulo limationetsa, ndipo litithandiza kubwerera kuti tiyenda m’njira yoyenera, ndipo limatithandiza kukhala m’njira yoyenera. Ahebri 4:12 atiuza kuti Mau a Mulungu ndi amoyo komanso amphamvu napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m'mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima ndi kucotsa macimo. Masalmo anenanso za kusintha kwa umoyo pa Masalmo 119. Yoswa anauzidwa kuti kupambana kunali mukulingalira pa Mau a Mulungu usana ndi usiku ndi kumvera Mulungu. Iye anacita comweci ngakhale kuti zina zimene Mulungu ananena makamaka pamene anali kupita ku nkhondo, sizinaoneke kuti ndi zogwira maganizo pa gawo la kumenya nkhondo, koma cimeneci cinali Mfundo la cigonjetso pa nkhondo zonse my dziko la malonjezano.

Baibulo ndi cinthu cimene nthawi zambiri sitigwiritsa nchito mofikapo kuti tithandizike kwenikweni. Mwina tingoinyamula cake kupita nayo ku mapemphero, kapena kuwerenga cabe capital imodzi pa tsiku koma tilephera kuloweza mau ace ndi kulingalirapo mofikapo pa mauwo ndi kuwagwiritsa nchito mu umoyo wathu; tilephera kuulula macimo athu pamene Baibulo lititsusa kapena kuyamika Mulungu. Tikabwera pa nkhani ya Baibulo sitiligwiritsa nchito kwambiri, kapena timaligwiritsa nchito mopitilira. Mwina tingotengako zotithandiza pa umoyo wa uzimu wa tsiku (koma sitikudya kuti tikhale ndi moyo wa masiku onse, kuti tikhale a Kristu athanzi), kapenanso timaligwiritsa nchito kwambiri koma tilephera kulingalirapo pa mauwo kuti tikhale aumoyo wa uzimu.

Ndicofunikira kuti ngati simunayambe kuwerenga ndi kuloweza Mau a Mulungu muyenera kuyamba kucita tero. Ena amaciona ndithu cofunikira ndipo iwo amalemba pena pake. Onetsetsani kuti simuwerenga cabe Mau ai, koma kuti mukawerenga mulemba pena pake, mwina mu buku lina, cimene mwamva ndi kutengapo pa Mau amene mwawerenga. Ena amasunga mapemphero yao ya kwa Mulungu kupempha Mulungu kuti awasinthe iwo pa mbali zofunikazo zimene Mulungu walankhula nao. Baibulo ndico cida cimene Mzimu Woyera amagwiritsa nchito mu miyoyo yathu (Aefeso 6:12-18), mbali yofunikira kwambiri pa zigawo za zida zofunikira pa kumenya nkhondo ya uzimu.

Cacitatu cina pa nkhondo yakulimbana ndi ucimo, ndi pemphero. Akristu kawirikawiri amanena za kufunikira kwa pemphero koma saligwiritsa nchito kwambiri. Timakhala ndi misonkhano ya mapemphero, nthawi yakupemphera ndi zina, koma ife lero pemphero sitiligwiritsa nchito monnga anzathu mu mpingo wakalero woyamba (Macitidwe 3:1; 4:31; 6:4; 13:1-3). Paulo anena za umo anapempherera anthu amene iye analalikira kwa iwo. Mulungu watipatsa malonjezano okoma pa nkhani yokhuza pemphero (Mateyu 7:7-11; Luka 18:1-8; Yohane 6:23-27; 1 Yohane 5:14-15), ndipo Paulo anenanso za kufunikira kwace kwa pemphero pa kukonzekera nkhondo ya uzimu (Aefeso 6:18).

Kodi pemphero ndilofunikira kotani pakugonjetsa cimo pa umoyo wathu? Pali mau amene usiku uja mu munda wa Getsemane, Kristu anauza Petro, iyeyo asanamukane Iye. Pamene yesu akupemphera, Petro akugona. Yesu amuutsa iye nati, “Cezerani ndi kupemphera, kuti mungalowe m'kuyesedwa: mzimutu uti wakufuna, koma thupi liri lolefuka” (Mateyu 26:41). Momwemo ifenso tili ngati Petro, tifuna kucita coyenera koma thupi lipezeka kuti ilibe mphamvu. Tifunika kulondola ciphunzitso ca Mau a Mulungu, kufunafuna, kugogoda ndi kufunsabe – ndipo Iye adzatipatsa mphamvu imene tifuna (Mateyu 7:7). Pemphero si magiki ai. Pemphero ndikungobvomereza kulephera kwathu pamaso pa Mulungu ndi kumuyamika Iye cifukwa ca mphamvu yace ndi kutembenukira kwa Iye kuti atipatse mphamvu yakucita cifuniro cace osati kucita monga mwa kufuna kwathu ai (1 Yohane 5:14-15).

Cacinai cofunikira pa nkhondo yakulimbana ndi kugonjetsa cimo m’kacisi, ndi kukhala m’ciyanjano ndi abale onse okhulupirira. Pamene Yesu anatumiza ophunzira ace, anawatuma iwo awiri-awiri (Mateyu 10:1). Anchito za amishoni mu buku la Macitidwe naonso sanapite pa yekha pa yekha ai, koma anapita awiri kapena monga mwa gulu. Yesu atilamulira ife kuti tisaleke kusonkhana kwathu pamodzi ndi kulimbikitsana wina ndi mzace, m’cikondi ndi pa nchito zabwino (Ahebri 10:24). Atiuza kuti tiulule macimo athu kwa ena (Yakobo 5:16). Mu nzeru za mu Cipangano Cakale, atiuza kuti citsulo cimanola citsulo cinzace ndipo munthu amanolanso munthu mzace (Miyambo 27:17). Mukukhala ambiri muli mphamvu (Mlaliki 4:11-12).

Akristu ambiri amapeza kuti akahala ndi mzao wabwino cimakhala cosavuta kugonjetsa macimo. Kukhala ndi munthu wina amene utha kulankhula naye, kupemphera naye pamodzi, kulimbikitsana, kapena kudzudzulana ndi cinthu ca mtengo wapatali. Kuyesedwa kumadza kawirikawiri pakati pa anthu ife (1 Akorinto 10:13). Kukhala ndi bwenzi kapena kukhala mugulu labwino citha kutithandiza ife pa zambiri za umoyo wathu ndi kutilimbikitsa pamene tifuna kugonjetsa macimo ovutitsa.

Nthawi zina cigonjetso cimadza mofulumira. Nthawi zina, cigonjetso cimacedwa kufika. Mulungu alonjeza kuti pamene tigwiritsa nchito zinthu zake, Iye adzabweretsa cisintho mu miyoyo yathu. Tikhoza kulimbika ndi kugonjetsa cimo cifukwa tidziwa kuti Mulungu afikilitsabe malonjezano ake pa ife.

EnglishBwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Ndingathe bwanji kugonjetsa cimo mu umoyo wanga wa CiKristu?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries