settings icon
share icon
Funso

Kodi ndingadziwe bwanji motsimikiza kuti ndikafa ndidzapita Kumwamba?

Yankho


Kodi mudziwa motsimikiza kuti muli ndi umoyo wosatha ndikuti mukafa mudzapita Kumwamba? Mulungu afuna kuti mukhale ndi citsimikizo! Baibulo likuta, “Izi ndakulemberani, kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha, inu amene mukhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu” (1 Yohane 5:13). Tingoyerekeza kuti lero lino munali kuima pamaso pa Mulungu ndipo mwafunsidwa motere: “Ncifukwa ninji ufuna kuti ndilole ulowe Kumwamba?” Munganene ciani? Simudzadziwa conena mwina. Cimene muyenera kudziwa ndikuti Mulungu atikonda ndipo Iye wapereka njira kuti ife tidziwe motsimikiza za umoyo wathu wopulumutsidwa ndi komwe tikakhale. Baibulo linena kuti, “Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wace wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha” (Yohane 3:16).

Coyamba tiyenera kumvetsa bvuto lotiletsa ife kufika Kumwamba. Bvuto ndi ili – umunthu wathu wa macimo umene ulekanitsa ubale pakati pa ife ndi Mulungu. Ndife ocimwa monga mwa cilengedwe komanso mwa kasankhidwe ka zinthu. “…pakuti onse anacimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu” (Aroma 3:23). Sitingadzipulumutse tokha ai. “Pakuti muli opulumutsidwa ndi cisomo cakucita mwa cikhulupiriro, ndipo ici cosacokera kwa inu: ciri mphatso ya Mulungu; cosacokera kunchito, kuti asadzitamandire munthu ali yense” (Aefeso 2:8-9). Tiyenera kulangidwa ndithu ku gehena. “Mphoto yace yaucimo ndi imfa” (Aroma 6:23).

Mulungu ndi woyera ndi wolungama ndipo ayenera kulanga cimo, koma atikonda zedi motero kuti anapereka umwai wacikhululukiro ca macimo athu. Yesu anati, “Yesu ananena naye, ine ndine njira, ndi coonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine” (Yohane 14:6). Yesu anatifera ife pa mtanda: “Pakuti Kristunso adamva zowawa kamodzi, cifukwa ca macimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu” (1 Petro 3:18). Yesu anaukitsidwa kwa akufa: “amene anaperekedwa cifukwa ca zolakwa zathu, naukitsidwa cifukwa ca kutiyesa ife wolungama” (Aroma 4:25).

Tero, tibwerere ku funso lathu – Yankho yake ndi iyi – Khulupirirani mwa Yesu Kristu ndipo mudzapulumutsidwa (Macitidwe 16:31). “Koma onse amene anamlandira iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lace” (Yohande 1:12). Mutha kulandira MPHATSO la umoyo wasatha. “Pakuti mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu” (Aroma 6:23). Mutha kukhala ndi umoyo wabwino ndi waphindu tsopano. Yesu anati, “Ndadza Ine kuti akhale ndi moyo, ndi kukhala nao wocuruka” (Yohane 10:10). Mutha kukakhala ndi umoyo wosatha pamodzi ndi Yesu Kumwamba pakuti Iye analonjeza kuti, “Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso” (Yohane 14:3).

Ngati mufuna kuvomereza yesu kukhala Mpulumutsi wanu ndi kulandira cikhululukiro kucokera kwa Mulungu, pali pemphero iyi imene mungapemphere. Kupemphera cabe pemphero ili kapena pemphero ina iriyonse sikungakupulumutseni. Ndikukhulupirira cabe mwa Yesu Kristu kumene kumapereka cikhululukiro ca macimo. Pemphero iyi ndi njira cabe moonetsera cikhulupiriro kwa Mulungu ndi kumuyamika cifukwa ca cikhululukiro ca macimo. “Mulungu, ndidziwa kuti ndakucimwirani ndipo ndiyenera kulangidwa. Koma Yesu anatenga cilango cimeneci cimene ndikadalandira motero kuti mwa kukhulupirira Iye ndi khululukidwa. Cipulumutso canga conse ciri m’manja a Inu, Yesu Kristu. Zikomo cifukwa ca cisomo canu ndi cikhululukiro canu! Amen!”

Kodi mwapanga ganizo la Khristu chifukwa cha zimene mwawerenga pano? Ngati ndi choncho, chonde sindikizani batani la “Ndavomera kulandira Khristu lero” pansipa.

EnglishBwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi ndingadziwe bwanji motsimikiza kuti ndikafa ndidzapita Kumwamba?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries