settings icon
share icon
Funso

Kodi domgosolo la chipulumutso ndilotani / njira ya chipulumutso?

Yankho


Muli ndi njala? Osati njala ya chakudya, koma muli ndi njala ya china chake chochuluka m’moyo mwanu? Pali china chake mkatikati mwanu chimene sichikhutitsidwa? Ngati ndi choncho, Yesu ndiye njira! Yesu anati, “Ine ndine mkate wamoyo. Amene adza kwa ine sadzamva njala, ndi iye akhulupilira mwa ine sadzamva ludzu” (Yohane 6:35).

Kodi mwasokonekera? Kodi simukupeza njira kapena cholinga m’moyo? Zikuoneka ngati wina wake wazimitsa kuunika ndipo simukupeza poyatsira? Ngati ndichoncho, Yesu ndiye njira! Yesu anati, “Ine ndine kuunika kwa dziko. Amene adza kwa ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala ndi kuunika kwa moyo” (Yohane 8:12).

Kodi mumamva ngati mwatsekeredwa kunja kwa moyo? Munayesapo zitseko zambiri, koma ndikumangopeza kuti kuseri kwake kulibe kanthu ndiponso kopanda ntchito? Kodi mukuyang’ana polowera ku moyo wokwanitsidwa? Ngati ndi choncho, Yesu ndiye njira! Yesu anati, “Ine ndine khomo; Amene adutsa kudzera mwa ine adzapulumutsidwa. Adzalowa ndi kutuluka, ndikupeza msipu” (Yohane 10:9).

Kdi anthu ena amakonda kukukhumudwitsani? Kodi ubale wanu wakhala osaya ndi opanda kanthu? Kodi zimaoneka ngati aliyense akuyesa kupeza mwayi pa inu? Ngati ndi choncho, Yesu ndiye njira! Yesu anati, “Ine ndine mbusa wabwino. Mbusa wabwino amayika moyo wake pa nkhosa. Ndine mbusa wabwino; Ndimadziwa nkhosa yanga ndipo nkhosa yanga imandidziwa Ine” (Yohane 10:11,14).

Mmasinkhasinkha chomwe chimachitika moyo uno ukatha? Mwatopa kukhalira moyo wanu pa zinthu zomwe zimawola kapena kuchita dzimbiri? Kodi nthawi zina mumakaikira ngati moyo uli ndi tanthauzo? Kodi mukufuna kukhala ndi moyo mukafa? Ngati ndi choncho, Yesu ndiye njira! Yesu anati, “Ine ndine kuuka ndi moyo. Yense wokhulupilira mwa ine adzakhala ndi moyo, ngakhale atafa; ndipo yense ali ndi moyo ndikukhulupilira mwa ine sadzafa” (Yohane 11:25-26).

Kodi njira ndi chiyani? Kodi choonadi ndi chiyani? Kodi moyo ndi chiyani? Yesu anayankha nati, “Ine ndine njira ndi choonadi ndi moyo. Palibe adza kwa Atate koma mwa ine” (Yohane 14:6).

Njala imene mumamva ndi njala ya uzimu, ndipo ndi Yesu yekha amene angathane nayo. Ndi Yesu yekha amene angachotse mdima. Yesu ndi khomo la kumoyo wokwanitsidwa. Yesu ndi mzanu ndi m’busa amene mwakhala mukumufuna. Yesu ndi moyo – m’moyo uno komanso wotsatirawo. Yesu ndi njira ya chipulumutso!

Chifukwa chimene mumvera njala, chifukwa chimene muoneka wosochera mu mdima, chifukwa chimene simungapeze cholinga m’moyo, ndichakuti munasiyana ndi Mulungu. Baibulo limatiuza kuti tonse tinachimwapo, ndipo tinadzichotsa kwa Mulungu (Mlaliki 7:20; Aroma 3:23). Kupanda kanthu mumtima mwanu ndi kusowa Mulungu m’moyo mwanu. Tinalengedwa kukhala pa ubale ndi Mulungu. Chifukwa cha machimo athu tinadzipatula ku ubale umenewu. Kuipitsitsa kwake, tchimo lathu lidzatipangitsa ife kupatukana ndi Mulungu kunthawi zosatha, m’moyo uno komanso winawo (Aroma 6:23; Yohane 3:36).

Kodi vuto limeneli lingathetsedwe bwanji? Yesu ndi njira! Yesu atadzitengera Iye yekha machimo athu (@ Akorinto 5:21). Yesu anafa m’malo mwathu (Aroma 5:8), kutenga chilango chimene chimayenera ife. Masiku atatu atatha, Yesu anauka kwa akufa, kutsimikiza kugonjetsa kwake kwa tchimo ndi imfa (Aroma 6:4-5). Ndi chifukwa chiyani Iye anachita izi? Yesu anayankha funso limenelo Iye mwini: “Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi,chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake” (Yohane 15:13). Yesu anafa ndicholinga chakuti tikhale ndi moyo. Ngati tiyika chikhulupiliro chathu mwa Yesu, kukhulupilira kuti imfa yake inali malipiro a machimo athu, machimo athu onse akhululukidwa ndikutsukidwa. Pakutero tidzakhutitsa ku njala ya uzimu. Kuunika kudzayatsidwa. Tidzakhala ndi mwayi wokhala ndi moyo wokwanitsa. Tidzawadziwa amzathu ndi abusa abwino. Tidzadziwa kuti tidzakhala ndi moyo tikadzafa – moyo wosatha wouka kwa akufa kumwamba ndi Yesu!

“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero kuti anapereka mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wokhulupilira Iye asatayike koma akhale nawo moyo wosatha” (Yohane 3:16).

Kodi mwapanga ganizo la Khristu chifukwa cha zimene mwawerenga pano? Ngati ndi choncho, chonde sindikizani batani la “Ndavomera kulandira Khristu lero” pansipa.

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi domgosolo la chipulumutso ndilotani / njira ya chipulumutso?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries