Cimacitika nciani potsatira imfa?


Funso: Cimacitika nciani potsatira imfa?

Yankho:
Pakati pa okhulupirira Yesu, pali kusiyana maganizo kwa kukulu pa kumvetsa cocitika potsatira imfa. Ena akhulupirira kuti potsatira imfa, aliyense “amagona” kufikira nthawi ya ciweruzo, pamene aliyense adzapita ku moyo wosatha kapena kucionongeko. Ena akhulupirira kuti munthu akangokufa, nthawi yomweyo aweruzidwa ndipo apita kumalo kumene ayenera kupezeka. Ena akuti munthu akafa, moyo/mzimu wake umatumizidwa kumalo “aciyembekezo” kumwamba kapena kucionongeko, kuyembekezera ciukitso, ciweruzo cotsiriza ndi kutumizidwa kumalo kumene miyoyo idzakhala kwa muyaya. Koma, kodi Baibulo inenapo ciani pa comwe cimacitika potsatira imfa?

Coyamba, kwa okhulupira mwa Yesu Kristu, Baibulo inena kuti okhulupirira akafa miyoyo/mizimu yao imatengedwa kumwamba, cifukwa anthuwa macimo yao akhululukidwa polandira Yesu Mpulumutsi (Yohane 3:16, 18, 36). Kwa okhulupirira, imfa ndi kusiyana ndi thupi koma kupezeka pamodzi ndi Ambuye (2 Akorinto 5:6-8; Afilipi 1:23). Koma m’malo ena monga pa 1 Akorinto 15:50-54 ndi pa 1 Atesalonika 4:13-17 anena za kuukitsidwa kwa okhulupirira ku kupatsidwa kwa matupi atsopano aulemerero kwa iwo. Ngati okhulupirira apita kukakhala ndi Yesu akangokufa, ndiye kuti nchito ya ciuukitso ndi ciani? Cioneka kuti pamene miyoyo/mzimu ya okhulupirira imapita kukakhala ndi \yesu nthawi yomweyo akangokufa munthuyo, thupi lace likhala m’manda “kugona.” Pa kuukitsidwa kwa okhulupirira, matupi ao aukitsidwa, nalandira ulemerero ndipo adzayanjanitsidwa ndi moyo/mzimu wao. Kuyanjanitsidwa uku kwa thupi la ulemelero ndo mzimu ndiwo adzakhala matupi a okhulupirira ku nthawi zosatha ku mwamba kwatsopano ndi pansi patsopano (Chibvumbulutso 21-22).

Caciwiri, kwa iwo onse amene sakhulupirira Yesu Kristu ngati Mpulumutsi wao, imfa kwa iwo itanthauza cilango cosatha. Koma kwa okhulupirira, adzakhala ndi umoyo wosatha, ndipo cioneka kuti naonso osakhulupirira akafa amapita kumalo akuyembekezerako kuyembekezera ciukitso cotsiliza, ciweruzo ndi umoyo wosatha ku nthawi zonse. Luka 16:22-23 anena za munthu wolemera, wacuma kwambili amene anazunzidwa atangokufa. Chibvumbulutso 20:11-15 anena za kuukitsidwa kwa akufa onse osakhulupira, kuweruzidwa ku mpando wacifumu waukuru woyera, ndi kuponyedwa mu Nyanja ya moto. Osakhulupirira akangokufa, satumizidwa ku gehena (nyanja ya moto) pamenepo ai, koma amapita kumalo koyembekezerako ciweruzo ndi cilango cosatha. Koma ngakhale kuti osakhulupirira satumizidwa ku Nyanja ya moto nthawi yomweyo akafa, ngakhale malo awo akuyembekezerako si abwino ai. Wacuma uja analira nati, “Ndipo anakweza mau nati, Atate Abrahamu, mundicitire cifundo, mutume Lazaro, kuti abviike nsonga ya cala cace m'madzi, naziziritse lilime langa; pakuti ndizunzidwadi m'lawi ili la moto” (Luka 16:24).

Motero, munthu akafa, iye akhala kumalo “oyembekezerako” umoyo wosatha kapena cionongeko cosatha – Kumwamba kapena gehena. Pakuyembekezera kumeneku, pa ciukitso cotsiliza, malo ace adzasinthidwa. Malo enieni a komwe iye adzakhale ndiwo asinthika. Okhulupirira onse adzapatsidwa mpata wolowa Kumwamba ndi dziko latsopano (Chibvumbulutso 21:1). Iwo wosakhulupirira adzapita ku Nyanja ya cionongeko (Chibvumbulutso 20:11-15). Malo awiri amenewa, ndiwo malo othera komwe anthu adzakhala ku nthawi zosatha ndi ici cidzacitika pa cifukwa cakuti iwo anakhulupirira Yesu yekha kuti Iye ndiye Mpulumutsi kapena ai (Mateyu 25:46; Yohane 3:36).

English


Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa
Cimacitika nciani potsatira imfa?