settings icon
share icon
Funso

Cifukwa ninji sindiyenera kudzipha?

Yankho


Mitima yathu ipita kwa iwo onse amene tsopano ali ndi maganizo ofuna kudzipha okha. Ngati mufuna kutero tsopano, pali zambiri zozetsa zimenezo mwina mwasowekera ciyembekezo mu umoyo wanu, kapena pali zovuta zina. Mukhoza kuona monga muli m’dzenje ndipo mukukayika ngati mungathe kuona ciyembekezo pakati pa zinthu zimene mwakumana nazo. Mwina palibe munthu amene akuikako nzeru kufuna kuona za zimene mwapitamo kumbuyo uku, kapena palibe amene akumvetsa za moyo wanu. Mwina palibe phindu lokhala ndi moyo tsopano.

Muyenera kutenga nthawi ndi kulola kuti Mulungu akhale Mulungu wanu mu umoyo wanu tsopano lino, Iye adzakuonetsani ukulu wace, “palibe comulephera Mulungu” (Luka 1:37). Mwina zocita za umoyo wanu mu zaka zapita zikusautsani ndipo mukakhala mukumva cisoni motero kuti simuona tsogolo labwino. M’mene mutero mutha kukhala munthu wokwiyakwiya, wamaganizo oipa, wacizondo, wofuna kulanga ena, kapena wamantha kotero kuti simutha kukhala ndi ubale wofunikira cifukwa ca kuganizira ena.

Cifukwa ninji mufuna kudzipha? M’bale, zinthu zingaipe bwanji mu umoyo wako, pali Mulungu amene akonda anthu onse mosawerengera kulakwa kwao. Iye ayembekezera kukuthandzizani mu nyengo ya zovuta zimenezo ndi kukuonetsani zabwino. Iyeyu ndiye ciyembekezo copezekeratu. Dzina lake ndiye Yesu.

Yesu ameneyu, ndiye Mwana wa Mulungu, wopanda cimo, ndipo akhala ndi inu mu nthawi zonse, nthawi kuzunzika ndi kucititsidwa manyazi. Mneneri Yesaya analemba za Iye mu Yesaya 53:2-6 ndipo akutere za Yesu, “Iye ananyozedwa ndi kukanidwa” ndi anthu onse. Umoyo wace unadzaza ndi cisoni ndi kuzunzidwa. Koma mavuto amene Iye anayamula sanali ace koma a ife. Iye ananyamula zowawa zathu, ndi kusenza zisoni zathu; koma ife tinamuvesa wokhomedwa wokanthidwa ndi Mulungu, ndi wobvutidwa. Iye analasidwa cifukwa ca zolakwa zathu, natundudzidwa cifukwa ca mphulupulu zathu; cilango cotitengera ife mtendere cinamgwera Iye; ndipo ndi mikwingwirima yace ife taciritsidwa.

M’bale, Yesu analola zonsezi kuti macimo ako akhululukiridwe. Palibe kanthu macimo ako ndi oipa motani, dziwani kuti Iye ndi wokonzeka kukukhululukira ndi kukulandira. “…Ndipo undiitane tsiku la cisautso: Ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza” (Masalmo 50:15). Kulibe cimo limene Yesu angalephere kukhululukira. Ena mwa anthu amene anatumikira Mulungu anacita macimo oipa monga kupha (Mose), kupha ndi cigololo (Mfumu Davide), komanso kulakwa kwa ena monga (Mtumwi Paulo). Ngakhale umoyo wao unali tero, iwo anakhululukiridwa ndipo analandira umoyo watsopano ndi wochuluka mwa Ambuye. “Cifukwa cace ngati munthu ali yense ali mwa Kristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano!” (2 Akorinto 5:17).

Cifukwa ninji simuyenera kudzipha? M’bale, Mulungu ndi wokonzeka kukonza zimene “zaonongeka” mu umuyo wako umene ulinao tsopano, moyo umene ufuna kuupha tsopano. Mu Yesaya 61:1-3, Mneneri akuti, “Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende; ndikalalikire caka cokomera Yehova, ndi tsiku lakubwezera la Mulungu wathu; ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro; ndikakonzere iwo amene alira maliro m'Ziyoni, ndi kuwapatsa cobvala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, cobvala ca matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika.”

Bwerani kwa Yesu ndipo Iye adzakupatsani cimwemwe pamene mukhulupira Iye ndipo adzayamba nchito yatsopano mu moyo wanu. Iye alonjeza kukupatsani cimwemwe cimene mwataya ndi kukupatsani mzimu wakukuthandizani inu. Iye afunitsitsa mtima wanu wothyoka “Pakuti simukondwera ndi nsembe, mwenzi nditapereka; Nsembe yopsereza simuikonda. Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka;Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa” (Masalmo 51:12, 15-17).

Kodi udzalola Ambuye kukhala Mpulumutsi komanso Wokutsogolera? Adzatsogolera maganizo ako tsiku ndi tsiku – mwa Mau ake opezeka mu Baibulo. “Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; Ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe” (Masalmo 32:8). “Ndipo kudzakhala cilimbiko m'nthawi zako, cipulumutso cambiri, nzeru ndi kudziwa; kuopa kwa Yehova ndiko cuma cace” (Yesaya 33:6). Mwa Kristu, mudzakumanabe ndi zovuta koma mudzakhala ndi ciyembekezo. Iye ndiye bwenzi lathu “Koma liripo bwenzi lipambana ndi mbale kuumirira” (Miyambo 18:24). Cisomo ca Ambuye Yesu cikhale ndi inu pamene mupanga ciganizo canu.

Ngati mufunitsitsa kukhulupirira Yesu ngati Mpulumutsi wanu, nenani mau awa kwa Mulungu mu mtima mwana: “Mulungu, ndikufunani mu mtima mwanga. Ndikhululukireni macimo anga onse. Ndaika cikhulupiro canga conse mwa Yesu Kristu kuti Iyeyu ndiye Mpulumutsi wanga. Conde ndiyeretseni, ndiciritseni, ndikundipatsa cimwemwe mu moyo wanga. Zikomo cifukwa ca kundikonda ine komanso zikomo cifukwa ca imfa ya Yesu m’malo mwa ine.”

Kodi mwapanga ganizo la Khristu chifukwa cha zimene mwawerenga pano? Ngati ndi choncho, chonde sindikizani batani la “Ndavomera kulandira Khristu lero” pansipa.

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Cifukwa ninji sindiyenera kudzipha?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries