settings icon
share icon
Funso

Kodi cipulumutso citheka ndi cikhulupiriro cokha kapena cikhulupiriro ndi zinchito?

Yankho


Iyi ndi funso lofunikira kwambiri pakati pa ziphunzitso za ciKristu. Funso limeneli nabweretsa kupatukana (Reformation), pakati pa mpingo wa Ciroma ndi a Protestanti. Funso limeneli ndi mfungulo pakati pa cipembedzo copezeka m’Mau ndi zipembedzo zina. Kodi cipulumutso citheka ndi cikhulupiriro cokha kapena cikhulupiriro ndi zinchito? Kodi ndipulumutsidwa pokhulupirira Yesu cabe, kapena mwa kukhulupirira Yesu ndi kutsata zinthu zina?

Funso la cikhulupiriro cokha kapena cikhulupiriro ndi zinchito ioneka yobvuta cifukwa ca mau ena mu Baibulo amene ali ovuta kuwamvetsa. Taonani Aroma 3:28, 5:1 ndi Agalatiya 3:24 ndi Yakobo 2:24. Ena aona kusiyana pakati pa Paulo (cipulumutso cidzera mwa cikhulupiriro cokha) ndi Yakobo (cipulumutso cidzera mwa cikhulupiriro ndi zinchito). Paulo ananetsa momveka ndiponso mophunzitsa molimba kuti cilungamo cidzera mwa cikhulupiriro cokha (Aefeso 2:8-9), ndipo Yakobo aoneka kuti akunena kuti cilungamo cidzera mwa cikhulupiriro ndi zinchito. Kumvetsa vuto ili pafunika kumvetsa bwino cymene Yakobo akunena. Yakobo akukana cikhulupiriro conena kuti munthu atha kukhala ndi cikhulupiriro nalephera kucita nchito zabwino (Yakobo 2:17-18). Yakobo akutsimikiza mfundo lakuti cikhulupiriro coona mwa Kristu cisintha umoyo ndipo cikhala ndi nchito zabwino (Yakobo 2:20-26). Yakobo pano sakunena kuti cilungamo cidza mwa cikhulupiriro ndi zinchito ai, koma kuti munthu amenedi ali wolungamitsidwa ndi cikhulupiriro adzakhalanso ndi nchito zambwino mu umoyo wace. Ngati munthu anena kuti ndi wokhulupirira, koma alibe nchito zabwino mu umoyo wace, ameneyo alibe cikhulupiriro coona mwa Kristu (Yakobo 2:14, 17, 20 26).

Paulo anenanso cimodzimodzi mu zolembedwa zace. Cipatso cokoma cymene okhulupirira ayenera kukhala naco cachulidwa pa Agalatiya 5:22-23. Atangonena kuti tipulumutsidwa mwa cikhulupiriro, osati mwa zinchito (Aefeso 2:8-9), Paulo atiuza kuti tinalengedwa kucita nchito zabwino (Aefeso 2:10). Paulo ayembekezera kwambiri umoyo wosinthika kwa ife monga Yakobo: “Cifukwa cace ngati munthu ali yense ali mwa Kristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano” (2 Akorinto 5:17). Yakobo ndi Paulo sakangana muziphunzitso zao pa nkhani ya cipulumutso. Iwo akungokamba pa nkhani imodzi koma poiona m’mbali zosiyana. Paulo akunenetsa kuti cilungamo cibwera mwa cikhulupiriro cokha pamene Yakobo anenetsa kuti cikhulupiriro mwa m’Kristu woona ndi wabwino cimaonetsa nchito zabwino.

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi cipulumutso citheka ndi cikhulupiriro cokha kapena cikhulupiriro ndi zinchito?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries