settings icon
share icon
Funso

Kodi Baibulo linena ciani za kupereka ca khumi?

Yankho


Akristu ambiri amavutika pa gawo la cakhumi. Mumachalichi ena mau angolinga pa cakhumi. Pa nthawi imodzimodzi, Akristu ambiri nao amatseka matu ndipo safuna kucita monga mwa Mau pa kupereka kwa Ambuye. Cakhumi/kupereka ciyenera kubweretsa cimwemwe ndi madalitso. Mwacisoni kuti masiku alero zinthu siziri tero muchalichi.

Cikhumi cipezekanso mu Cipangano Cakale. Cakumi cinaperekedwa monga mwa lamulo lopatsidwa kwa Aisrayeli, iwo analamuliridwa kupereka cakhumi pa mbeu zimene iwo analima komanso cakhumi pa ziweto zao, izi zonse anazipereka kumalo opemphererako (Levitiko 27:30; Numeri 18:26; Deuteronomo 14:24; 2 Mbiri 31:5). Coonadi ndicakuti Lamulo linafuna iwo kupereka cakhumi m’magawo-magawo – cina ca a Levi, cina cogwiritsira nchito m’kacisi ndi pa zikondwerero zofunikira, cina ca pa nthaka lopanda conde – ndipo zonsezo totala yake inakhala ngati 23.3 pelesenti Ena amamvetsa cakhumi ca mu Cipangano Cakale kukhala ngati msonkho woperekedwa kuti ansembe ndi a Levi akwaniritse zofunikira pa nchito yakupereka nsembe zopsereza ndi zina zofunikira.

M’cipangano Catsopano sanena mofikiritsa za cakhumi cotero ai. Komanos palibe pamene anena za pelesenti, koma angonena kuti, “molinganiza ndi colowa cace kapena kuphindula kwace” (1 Akorinto 16:2). Ena anthu atengera za 10 pelesenti yaku Cipangano Cakale kukhala ngati cakhumi ndipo aika omwewo kukhala ngati “muyeso woikika” wa Akristu pa kupereka.

Mu Cipangano Catsopano anenanso za kufunikira ndi zabwino zopezeka pa kupereka. Tiyenera kupereka monga m’mene tikhoza. Nthawi zina cimeneco citanthauza kupereka koposa pa khumi; nthawi zina cimeneco citha kutanthauza kupereka mocepekera pa khumi. Zonse ziima pa momwe Mkristu amvetsera ndi kukwanitsira komanso zofuna za thupi la Kristu. Mkristu aliyense ayenera kupemphera mwakuya ndi kufunsira nzeru ya Mulungu pa gawo ili lokhuza cakhumi komanso kuti apereke zingati (Yakobo 1:5). Pa izi zonse, zakhumi zonse ndi zopereka zonse ziyenera kuperekedwa mwangwiro ndi mkhalidwe wopembedza Mulungu ndi kuthandiza ena mwa Ambuye. “Yense acite monga anatsimikiza mtima, si mwa cisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera” (2 Akorinto 9:7).

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi Baibulo linena ciani za kupereka ca khumi?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries