settings icon
share icon
Funso

Kodi Baibulo linena ciani pa kumwa zoledzeretsa / vinyo (waini)? Kodi ndi cimo kwa Mkristu kumwa zoledzeretsa / vinyo (waini)?

Yankho


Mau alipo ambiri mu Baibulo okhudza nkhani ya kumwa zoledzeretsa (Levitiko 10:9; Numeri 6:3; Deuteronomo 29:6; Oweruza 13:4, 7, 14; Miyambo 20:1; 31:4; Isaiah 5:11, 22; 24:9; 28:7; 29:9; 56:12). Ngakhale ziri tero, Mau a Mulungu saletsa Mkristu kumwa mowa, waini kapena zakumwa zina zimene mkati mwa izo muli pelesenti ya kachasu. Ndime zina zigwirizana ndi zakumwa zoledzeretsa pothandizira thupi. Mlaliki 9:7 atero, “Tiye, idya zakudya zako mokondwa, numwe vinyo wako mosekera mtima; pakuti Mulungu wabvomerezeratu zocita zako.” Masalmo 104:14-15 atero kuti Mulungu amapatsa vinyo, “umene ukondweretsa mitima ya anthu.” Amosi 9:14 anenenso za kumwa kwa vinyo, wocokera ku dzipatso za m’munda wace munthu kukhala ngati dalitso la Mulungu. Yesaya 55:1 akutere mobvomekeza, “Inde, mugule vinyo ndi mkaka…”

Cimene Mulungu alamulira a Kristu pa nhani ya kumwa zoledzeretsa ndi cakuti munthu asaledzere (Aefeso 5:18). Baibulo lidana nako kuledzera ndi zotulukamo m’kuledzera (Miyambo 23:29-35). Akristu alamulidwa kuti asamalire matupi ao, asdetsedwe konse (1 Akorinto 6:12; 2 Petro 2:19). Kumwa zoledzeretsa mopitilira malire ndiko kukhala wokodwa ndipo wotero adzolowera. Akristu aletsedwa kucita cili conse cimene cingakhumudwitse ena a Kristu kapena kupereka iwo ku ucimo kapena kuwazunza maganizo (1 Akorinto 8:9-13). Mwa mau ndi ziphunzitso zonsezi, cidzakhala cobvuta kwambiri kwa Mkristu aliyense kunena kuti iye ali kumwa kwambiri ndi colinga coti alemekeze Mulungu (1 Akorinto 10:31).

Yesu anasandulitsa madzi kukhala vinyo. Cioneka kuti pa nthwi imeneyo, Yesu anamwa vinyo (Yohane 2:1-11; Mateyu 26:29). Mu nthawi za mu Cipangano Catsopano, madzi sanali audongo kwambili. Kopanda zisamaliro zatsopano madzi akhala ndi dothi ndi tizilombo topezeka m’menemo kuononga. Ndipo zimenezo zipezekanso m’madzi a m’maiko ambili pa dziko pano, makamaka maiko osauka. Motero anthu ambiri pa nthawiyo anali kumwa vinyo cifukwa sunali ndi tizombo monga madzi ai. Mu 1 Timoteo 5:23, Paulo auza Timoteo kuti sayenera kumwa madzi amene (mwina ankamubweretsera matenda am’mimba) koma kuti azimwa vinyo. Panthawiyo vinyo unali ndi cotupisa (kukhala ndi kachasu mkati kapena wosasa), koma osati monga momwe umakhalira masiku ano. Ndizoona kuti anali madzi za zipatso za mpesa, koma sizoona kunena kuti zimenezo – vinyo wa nthwiyo ndi wa nthawi za lero – ndiwofanana. Mau a Mulungu saletsa Mkristu kumwa mowa, vinyo kapena waini kapena cakumwa cina cili conse cokhala ndi kachasu mkati mwace. Kachasu pa iwo okha, komanso mwa iwo okha ulibe cimo. Mkristu sayenera kuledzera kapena kuzolowera kumwa zoledzeretsa, iye ayenera kudziletsa kutero (Aefeso 5:18; 1 Akorinto 6:12).

Coledzeretsa, comwedwa pang’ono cabe siciononga kapena kuzolowereka. Madotolo amatero kuti kumwako cabe pang’ono kumathandiza thupi, makamaka mtima. Kumwako pang’ono zoledzeretsa zikhala ngati ufulu wa Mkristu. Kuledzera ndi kumwa mobwerezabwereza ndi cimo. Koma pa cifukwa za zimene Baibulo linena zokhuza zakumwa zoledzeretsa ndi zotulukamo munthu akamwa, cimakhala capafupi kwa muthuyo kugwa m’cimo la kupitiliza kungokumwa, ndiponso cikhalanso capafupi kukhumudwitsa ena kapena kugwa m’macimo, motero ndicofunikira kwa Mkristu kudziletsa kumwa zoledzeretsa.

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi Baibulo linena ciani pa kumwa zoledzeretsa / vinyo (waini)? Kodi ndi cimo kwa Mkristu kumwa zoledzeretsa / vinyo (waini)?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries