settings icon
share icon
Funso

Azibusa acikazi / wolalikira? Kodi Baibulo linena ciani pa akazi mu ulaliki?

Yankho


Ngati pali nkhani ya moto lero mu chalichi ndi nkhani ya akazi kukhala ndi maudindo kufikira kukhala wolalikira. Motero sipafunika kuiona nkhani iyi ngati nkhondo pakati pa amuna ndi akazi. Pali akazi amene akhulupira kuti akazi anzao asatumikire ngati alaliki kapena abusa ndikuti Baibulo linaika malire pa maudindo amene akazi atha kucita, ndipo palinso amuna amene akhulupira kuti akazi atha kusenza udindo wina uliwonse mu chalichi kufikira kukhala mlaliki. Iyi sinkhani cabecabe ai, koma igona pa m’mene anthu amasulira Mau a m’Baibulo.

Mau a Mulungu akuti, “Mkazi aphunzire akhale wacete m'kumvera konse. Koma sindilola ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna; komatu akhale cete.” (1 Timoteo 2:11-12). Mu chalichi Mulungu apereka maudindo osiyana kwa amuna ndi akazi. Ici ndi cifukwa ca cilengedwe cao komanso m’mene ucimo unalowera m’dziko lapansi (1 Timoteo 2:13-14). Mulungu kupyolera mwa mtumiki Paulo, aletsa akazi kusenza maudindo ophunzitsa ndi kukhala ndi kulamulira amuna pa udindo wa zauzimu. Izi pamodzi ndi kuikapo akazi kutumikira pa udindo wa ulaliki pakati pa amuna, ndipo ndicodziwika kuti udindo umenewu uli ndi gawo lophunzitsa amuna komanso kukhlala ngati wansembe pakati pao.

Pali zambili zokangana ndi ubusa wa akazi mu mpingo. Codziwika bwino kwambiri ndi mau a Paulo oletsa akazi kuphunzitsa cifukwa m’zaka zoyambazo, akazi analibe maphunziro. Koma pa 1 Timoteo 2:11-14 sakambapo nkhani za maphunziro ai. Ngati kuti maphunziro anali cofunikira coyamba pa nchito imeneyi, ambiri a ophunzira a Yesu sakadaloledwa kutsata Iye. Cina cokaniza pano ndicakuti Paulo anakaniza cabe akazi aku Efeso kuphunzitsa amuna (1 Timoteo analemberedwa kwa Timoteo, mtsogoleri wa mpingo waku Efeso). Efeso anali wadziwika cifukwa ca akacisi a Atermi, komanso akazi ndiwo anali mu ulamuliro za zipembezo za milungu ina zimenezi – motero ziganizo a akazi kukhala atsogoleri ndipo Paulo amanena za akazi omwewa aku Aefeso otsogolera zipembedzo za milungu yacabe ndipo Mpingo uyenera kukhala wasiyana ndi zimene zimacitikazo komweko. Koma tikaonetsetsa palibe pomwe mu buku la 1 Timoteo anenapo za Artemis komanso Paulo sanena za zocitika pakati pa iwo wopembedza Artemi kukhala ngati cifukwa coletsera mu 1 Timoteo 2:11-12).

Cacitatu pa nkhani iyi ndi cimene Paulo anena pokamba za amuna ndi akazi amubanja, osati amuna ndi akazi ena onse ai, koma iwo ali m’cikwati. Mau a ciGriki a “mkazi” ndi “mwamuna” mu 1 Timoteo 2 akhoza kuyerekezedwa kwa iwo okhala m’banja, koma, tanthauzo la mauwo litha kuposapo. Tikaonapo mwakuya, mauwo mu ciGriki agwiritsidwanso nchito mu vesi 8-10. Kodi amuna ababanja ndiwo okha oyenera kunyamula manja oyera mu mwamba kopanda kukwiya ndi makani (vesi 8). Kodi akazi okha okwatiriwa ndiwo ayenera kubvala bwino kwambiri, ndi kucita nchito zabwino, ndi kuyamika Mulungu (vesi 9-10)? Zonsezo ai. Apa, maversi 8-10, anena za amuna onse ndi akazi onse, osati cabe kwa iwo okhala m’banja. Palibe coonetsa kuti mauwo apa akhuza kuyerekezedwa kwa amuna ndi akazi apa banja mu vesi 11-14.

Mau ena amene amagwiritsidwa nchito pa nkhani iyi ya akazi kukhala ansembe kapena kuti abusa, yalodzera ku mau ya akazi amene anali ndi udindo mu Baibulo, makamaka monga, Miriamu, Debora, ndi Hulda mu Cipangano Cakale. Ndizoona kuti akazi amenewa anasankhidwa ndi Mulungu kuti akacite nchito yapadera yopatulikira iwo kuicita ndipo iwo akhala ngati akazi amene titha kuyanganirako cifukwa ca cikhulupiriro cao, kulimbika kwao ndi utsogoleri wao. Koma udindo wa akazi mu Cipangano Cakale si ukhuzana kwenikweni ndi nkhani ya akazi kukhala abusa mu mpingo. Makalata amu Cipangano Catsopano aonetsa kusintha kwa zinthu pakati pa anthu a Mulungu – mu mpingo, mu thupi la Kristu – ndipo kusinthaku kukhuzana ndi momwe magawo a mpingo aliri, osati zokhuzana ndi dziko la Aisrayeli, kapena ena anthu a mu Cipangano Cakale.

Pali maganizo ena amene amagwiritsidwa nchito polowapo kwambiri pa nkhani imeneyi, mogwiritsa nchito anthu akazi awa, Febe ndi Priskila mu Cipangano Catsopano. Mu Macitidwe 18, Priskila ndi Akula aonetsedwa kukhala atumiki okhulupirira a Kristu. Dzina la Priskila lichulidwa poyamba, mwina kuonetsa kuti iye anali wocitacita koposa mwamuna wake (Akula) mu utumiki wa Kristu. Kodi priskila ndi mwamuna wace anaphunzitsa za uthenga wabwino wa Yesu Kristu kwa Apolo? Inde, mu nyumba yao iwo anatero, “anamtenga, namfotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa” (Macitidwe 18:26). Kodi Baibulo linena kuti Priskila anali ndi mpingo kapena kuti ankaphunzitsa pagulu kapenanso kuti iye, Priskila, anakhala mtsogoleri wa zauzimu mu mpingo wa oyera mitima? Ai! Monga m’mene tidziwira, Priskila sanagwepo nao pa zotero mosiyana ndi mau apa 1 Timoteo 2:11-14.

Mu Aroma 16:1, mkazi wochedwa Febe anapatsidwa udindo wokhala “mtumiki” (kapena “kapolo”) wa mkacisi ndipo Paulo anena ndi kuyamikira za udindo umenewu. Koma mkazi wina wochedwa, Priskila, mulibe mu Mau a Mulungu coonetsa kuti Febe anali m’busa kapena mphunzitsi wa amuna mu mpingo. “Kukwaniritsa kuphunzitsa” ndi udindo umene umapatsidwa kwa akulu oyanganira mu mpingo koma osati azitumiki (1 Timoteo 3:1-13; Tito 1:6-9).

Mau opezeka pa 1 Timoteo 2:11-14 yapereka cifukwa cimene akazi satha kukhala azibusa mwathunthu. Vesi la 13 iyamba motere, “pakuti,” kupereka “codzetsa” kapena “coyambitsa” mau a Paulo mu mavesi 11-12. Cifukwa ninji akazi sayenera kuphunzitsa kapena kukhala ndi udindo wa zauzimu wotere pakati pa amuna? Cifukwa cake ndi kuti, “Pakuti Adamu anayamba kulengedwa, pamenepo Hava; ndipo Adamu sananyengedwa, koma mkaziyo ponyengedwa analowa m'kulakwa” (vesi 13-14). Mulungu analenga Adamu poyamba, ndipo potsatira analenga Hava kukhala “womthandiza” wa Adamu. Cilengedwe cimeneci ciri ndi momwe zinthu ziyenera kukhalira m’banja (Aefeso 5:22-23) komanso mu mpingo wonse.

Cifukwa cakuti Hava ananyengedwa, cikhalanso copatsidwa pa 1 timoteo 2:14 kuti mkazi asacite nchito ya ulaliki wa ubusa kapena kukhala ndi udindo wa zauzimu pakati pa amuna. Izi, sizitanthauza kuti akazi sangathe kutero ai kapena kuti ndi anthu apafupi kunamizidwa ndi amuna ai. Ngati akazi onse ngwapafupi kunamizidwa (kunyengedwa) bwanji iwo aloledwa kuphunzitsa ana (amena ndi apafupi kunamiza) ndi akazi ena (amene ayelekezedwa ngati kukhala osavuta kunamiza)? Mau pano angonena cabe kuti akazi sayenera kuphunzitsa amuna kapena kukhala ndi udindo wa za uzimu pakati pa amuna cifukwa Hava ananamizidwa. Mulungu wasankha amuna kuwapatsa udindo wofunikira wakuphunzitsa mkacisi.

Akazi amabiri amacita bwino pa mphatso monga za kucezerana, kuonetsa zacifundao, kuphunzitsa, ulaliki ndi kuthandiza ena. Nchito zambiri mu mpingo ziri m’manja ya azimai. Iwo mkacisi saletsedwa kupemphera pagulu kapena kunenera (1 Akorinto 11:5), koma aletsedwa kukhala ndi udindo wakuphunzitsa za uzimu pakati pa amuna. Koma palibe mu Baibulo pamene aletsa kuti mkazi asagwiritse nchito za cipatso ca Mzimu Woyera (1 Akorinto 12). Akazi, monganso amuna naonso aitanidwa kucita nchito ya kukopa ena, konetsa nchito za cipatso ca Mzimu Woyera (Agalatiya 5:22-23), ndi kulalikira uthenga wabwino kwa otaika (Mateyu 28:18–20; Macitidwe 1:8; 1 Petro 3:15).

Mulungu anaika kuti amuna atumikire mu maudindo a uphunzitsi pa za uzimu mu chalichi. Ici sicifukwa cakuti amuna ndi opambana pa nkhani yophunzitsa ai kapena kuti akazi ali pansi pa amuna ai, si kapenanso kuti kapena amuna ndi anzeru ai. Ici ndi cifukwa ca m’mene Mulungu anapangila kuti mpingo uzigwirira nchito zake. Amuna akhale citsanzo pa zauzimu – mu umoyo wao ndiponso kupyolera mwa mau ao. Akazi akhale ndi udindo umene uli wocepekera mwa nchito. Akazi afulumizidwanso kuphunzitsa akazi anzao (Tito 2:3-5). Baibulo sililetsa akazi kuphunzitsa ana. Iwo, akazi, aletsedwa cabe kuphunzitsa kapena kukhala ndi udindo wa uzimu wakulamulira amuna. Izi kuikaponso akazi kukhala alaliki kwa amuna. Kutero sindiko kuti akazi alibe phindu ai, koma iwo apatsidwa nchito yopambana ndi yobvomerezedwa mu pulano la Mulungu ndipo awapatsa iwo mphatso zowathandiza pa nchitozo.

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Azibusa acikazi / wolalikira? Kodi Baibulo linena ciani pa akazi mu ulaliki?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries