settings icon
share icon
Funso

Okapulumutsidwa kamodzi, ukhalabe wopulumutsidwa?

Yankho


Munthu akangopulumutsidwa kamodzi ndiko kuti ameneyo akhalabe wopulumutsidwa? Anthu akadziwa Kristu kukhala Mpulumutsi wao, iwo amalowa mu ubale ndi Mulungu ndipo Mulungu amawalonjeza umoyo wosatha. Pali mavesi ambiri a Mau a Mulungu amene anena ndi kutsimikizira za ici.

(a) Aroma 8:30 “Ndipo amene Iye anawalamuliratu, iwo anawaitananso; ndimo iwo amene Iye anawaitana, iwowa anawayesanso olungama; ndi iwo amene Iye anawayesa olungama, iwowa anawapatsanso olemerero.” Vesi iri litiuza kuti nthawi imene Mulungu watisankha, cimakhala monga kuti tikhala mu ulemerero wace pamodzi ndi Iye kumwambako. Palibe cimene cingaletse okhulupirira ngakhale tsiku limodzi kukhala mu ulemerero cifukwa Mulungu anakonzeratu kale zonsezo. Munthu akalungamitsidwa, cipulumutso cace cimapatsidwa – iye akhalabe mu citetezo cifukwa ulemerero wace ukhala wokhazikika kumwamba.

(b) Paulo akufunsa mafunso awiri olimba pa buku la Aroma 8:33-34 “Ndani adzaneneza osankhidwa a Mulungu? Mulungu ndiye ameneawayesa olungama; ndani adzawatsutsa? Kristu Yesu ndiye amene adafera, inde makamaka, ndiye amene adauka kwa akufa, amene akhalanso pa dzanja lamanja la Mulungu, amenenso atipempherera ife.” Ndani amene adzabweretsa mlandu kwa osankhidwa ace a Mulungu? Palibe ngakhale m’modzi pakuti Yesu ndiye wotiimilirirako. Ndani adzatistutsa ife? Palibe ngakhale m’modzi, cifukwa Kristu, Iye amene anatifera ife, ndiye yekha amene amatsutsa. Pano tiri ndi omirira wina pa mlandu komanso oweruza mlanduwo.

(c) Okhulupirira akhala obadwa kwatsopano (kuyamba kwatsopano kukula) akakhulupirira (Yohane 3:3; Tito 3:5). Kwa Mkristu kutaya cipulumutso cake, ndiko kuti iye ayenera kucotsedwa pa kukula. Baibulo silipereka umboni kuti cipulumutso citha kucotsedwanso ngati capatsidwa.

(d) Mzimu Woyera akhala mwa okhulupirira onse (Yohane14:17; Aroma 8:9) ndipo muwabatize onse okhulupirira Mthupi la Kristu (1 Akorinto 12:13). Kwa okhulupirira kuti akhale osapulumutsidwa, ndiko kuti Mzimu Woyera “wamucokera” ndipo walekanitsidwa ndi thupi la Kristu.

(e) Yohane 3:15 mau anena kuti yense wakukhulupirira mwa Yesu “adzakhala ndi moyo wosatha.” Ngati ukhulupirira Yesu lero lino ndi kukhala ndi moyo wosatha, koma kuutaya mawa, ndiko kuti moyo umenewo siunali “umoyo wosatha” konse. Motero ukutaya cipulumutso cako, lonjezano la umoyo osatha mu Baibulo likhoza kukaikiridwa komanso ndiko kuti pamenepo pali colakwika.

(f) Potsirizira kwenikweni pa makani, ndiganiza kuti Mau anena bwino okha, “Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu ziripo, ngakhale zinthu zirinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale colengedwa cina ciri conse, sicingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi cikondi ca Mulungu, cimene ciri mwa Kristu Yesu Ambuye wathu” (Aroma 8:38-39). Kumbukira kuti Mulungu yemweyo amene anakupulumutsani ndiyemwenso adzakusungani. Tikapulumutsidwa kamodzi, tikhalabe opulumutsidwa. Cipulumutso cathu cikhalabe cosatha kapena cakuya!

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Okapulumutsidwa kamodzi, ukhalabe wopulumutsidwa?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries