settings icon
share icon
Funso

Kodi cipembedzo coona ndi citi kwa ine?

Yankho


Malo ambiri odyeramo, amatilola kugula cakudya monga momwe tifunira kuti cikhalire. Masitolo ena a zakumwa zotentha monga tiyi, amakhala ndi mitundu-mitundu ya zakumwazo. Ngakhale pamene tifuna kugula nyumba kapena galimoto timasankha imene iri ndi zinthu zimene tifunitsitsa. Sitikhale m’dziko m’mene zinthu zicitika kopanda zisankho ai. Chisankho cikhala cofunikira. Mutha kupeza ciriconse cimene mufuna monga mwa kufuna kwanu.

Kodi cipembedzo cimene inu mukondwera naco ndi citi? Nanga cipembedzo cimene ngakhale pamene mupemphera mukhala ndi ufulu m’maganizo, komanso sicifuna zambiri kucokera kwa inu monga zocita ndi zosacita ndi citi? Kodi cilipo kapena palibe? Cipembedzo ndi cinthu cimene munthu amasankha monganso angasankhile zinthu, monga ndiwo za masamba, ngati wapiti ku maliketi.

Pali mau ambiri a anthu ena amene afuna kuti ena adzipembedzedwa, ndiye ncifukwa ninji tiona anthu ena kutama Yesu m’malo motama mwina Muhammad kapena Confucius, Buddha, kapena Charles Taze Russell kapena Joseph Smith. Kodi sikuti njira zonse zipita Kumwamba? Kodi zipembedzo zonse sizolingana? Coonadi ndi cakuti sizonse zipembedzo zimene zilunjika Kumwamba, monganso ena amanena kut si zonse njira zimene zipita ku Indiana.

Yesu yekha amalankhula ndi mphamvu ya Mulungu popeza Iye yekha anagonjetsa imfa. Muhammad, Confucius, ndi ena onse kufikira tsopano, iwo ali m’manda mwao. Koma yesu, mwa mphamvu yace Iye anagonjetsa imfa atafa imfa yoopsa ndithu. Ali yense amene ali ndi mphamvu pa imfa, tiyenera kumudziwa munthuyo.

Umboni wosonyeza kuuka kwa Yesu ulipo wambiri wokwanira. Coyamba panali anthu mazana asanu (500) amene anamuona Iye atauka! Anthuwo ngoculuka kwambiri. Mau a anthu mazana asanu sangathe kuponderezedwa. Komanso pali nkhani yakuti m’manda m’mene anamuika Iye munalibe Iye. Iwo onse otsutsa Yesu akadakana nkhani ya kuuka kwace poonetsa thupi lace kwa anthu, koma iwo analibe thupi la Yesu popeza Yesu anali wa moyo, atauka ndithu! M’mandamo munalibe kanthu! Kodi ophunzira ace anali ataba thupi lace? Ai. Kuti zimenezo zakuba thupi lace zisacitike, kumandako kunali asilikari azida m’manja kulonda komweko. Komanso abwenzi ambiri a Yesu anali atathawa pamene Iye anamugwira ndi kupita naye kukapacikidwa, ndicosatheka kuti anthuwo akadagwebana ndi asilikari pofuna kutenga thupi la Yesu kumandako. Komanso iwo sanali okonzeka kuferapo pa nkhani yotero – monga m’mene ena anacitira mwacinyengo. Cidziwika ndi cakuti kuuka kwa Yesu Kristu sikungathe kukhala nkhani yobisa.

Mobwerezanso, ngati pali munthu amene ali ndi mphamvu pa imfa, ameneyo ayenera kudziwika. Yesu anaonetsera kupambana kwace pa imfa; motero tiyenera kumvera cimene Iye anena. Yesu akunena kuti ndiye njira ya cipulumutso (Yohane 14:6). Iye ndiye njira yokhayo yacipulumutso, zinazi si njira za cipulumutso.

Ndipo pa nthawi iyi Yesu anati, “Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu” (Mateyu 11:28). Dziko lino ndi lobvuta ndipo umoyo ukhoza kukhala obvutikanso. Ambiri a ife ndife okhumudwa komanso okwiya ndi zinthu zina za m’dziko. Mobvomereza kodi? Tsopano mufuna ciani? Kubwezera zinthu m’malo mwake kapena cipembedzo cabe? Mpulumutsi wa moyo kapena m’modzi wa “aneneri” amene anafa kale? Ubale woona kapena miyambo ina yake? Yesu sapikisana ndi wina – Iye yekha ndiye cisankho!

Yesu ndiye “cipembedzo” coona ngati mukufuna cikhululukiro ca macimo (Macitidwe 10:43). Yesu ndiye “cipembedzo” coona ngati mukufuna ubale weniweni ndi ophindulitsa pakati pa inu ndi Mulungu (Yohane 10:10). Yesu ndiye “cipembedzo” coona ngati mukufuna umoyo wosatha wakumwamba (Yohane 3:16). Ikani cikhulupiro canu mwa Yesu pokhala Mpulumutsi wanu; ndipo simudzakhumudwa ai! Khulupirirani Iye kuti adzakhululuka ndi kukucotserani macimo; ndipo simudzakhumudwa konse ai.

Ngati mufuna kukhala ndi “ubale woyenera” ndi Mulungu, pano pali pemphero. Kumbukirani, kuti kunena pemphero iyi kapena pemphero lina lirilonse sikudzakupulumutsani. Mupulumutsidwa pokhapo mukakhulupira mwa Yesu kuti ndiye Mpulumutsi wocotsera macimo. “Mulungu, ndidziwa kuti ndakucimwirani ndipo ndiyenera kulangidwa. Koma Yesu Kristu anatenga cilango ca macimo anga motero mwa kukhala ndi cikhulupiriro mwa Iye ndikhululukidwa. Ndiika cikhulupirira canga mwa Inu kuti ndipeze cipulumutso. Zikomo pa cisomo ndi cikhululukiro canu – cimene ciri mphatso ya umoyo wosatha! Amen!”

Kodi mwapanga ganizo la Khristu chifukwa cha zimene mwawerenga pano? Ngati ndi choncho, chonde sindikizani batani la “Ndavomera kulandira Khristu lero” pansipa.

English



Bwelerani ku peji lalikulu la Chichewa

Kodi cipembedzo coona ndi citi kwa ine?
Facebook icon Twitter icon Pinterest icon Email icon
© Copyright Got Questions Ministries